Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mafumu 2:7 - Buku Lopatulika

7 Koma uchitire zokoma ana aamuna aja a Barizilai wa ku Giliyadi, akhale pakati pa akudyera pa gome lako, popeza momwemo amenewo anandiyandikira muja ndinalikuthawa Abisalomu mbale wako.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Koma uchitire zokoma ana amuna aja a Barizilai wa ku Giliyadi, akhale pakati pa akudyera pa gome lako, popeza momwemo amenewo anandiyandikira muja ndinalikuthawa Abisalomu mbale wako.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 “Koma ana a Barizilai wa ku Giliyadi, uŵachitire zabwino ndi kuŵalola kuti azidya pamodzi nawe, poti adandichitira chifundo pamene adakumana nane nthaŵi imene ndinkathaŵa Abisalomu mbale wako.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 “Koma ana a Barizilai wa ku Giliyadi uwakomere mtima ndipo uwalole kuti akhale mʼgulu la anthu amene azidya pamodzi nawe. Pakuti anandisamalira pamene ndinkathawa mʼbale wako Abisalomu.

Onani mutuwo Koperani




1 Mafumu 2:7
15 Mawu Ofanana  

Koma undikumbukire ine m'mene kudzakhala bwino ndi iwe, ndipo undichitiretu ine kukoma mtima: nunditchule ine kwa Farao, nunditulutse ine m'nyumbamu:


Pakuti nyumba yonse ya atate wanga inali anthu oyenera imfa pamaso pa mbuye wanga mfumu; koma inu munaika mnyamata wanu pakati pa iwo akudya pa gome lanu. Kuyenera kwanga nkutaninso kuti ndikaonjezere kudandaulira kwa mfumu?


Ndipo uzimlimira munda wake, iwe ndi ana ako ndi anyamata ako; nuzibwera nazo zipatso zake kuti mwana wa mbuye wako akhale ndi zakudya; koma Mefiboseti, mwana wa mbuye wako, adzadya pa gome langa masiku onse. Ndipo Ziba anali nao ana aamuna khumi ndi asanu, ndi anyamata makumi awiri.


Ndipo Davide ananena naye, Usaopa, pakuti zoonadi ndidzakuchitira kukoma mtima chifukwa cha Yonatani atate wako; ndi minda yonse ya Saulo ndidzakubwezera, ndipo udzadya pa gome langa chikhalire.


Nasintha zovala zake za m'kaidi, namadya iye mkate pamaso pake masiku onse a moyo wake.


Ndi kunena za chakudya chake, panali chakudya chosalekeza chopatsidwa kwa iye ndi mfumu, tsiku lililonse gawo lake, masiku onse a moyo wake.


Ndi ana a ansembe: ana a Habaya, ana a Hakozi, ana a Barizilai, amene anadzitengera mkazi wa ana aakazi a Barizilai Mgiliyadi, natchedwa dzina lao.


Mnzako, ndi mnzake wa atate wako, usawasiye; usanke kunyumba ya mbale wako tsiku la tsoka lako; mnansi wapafupi aposa mbale wakutali.


Ndipo anapindula zovala zake za m'ndende, ndipo sanaleke kudya pamaso pake masiku onse a moyo wake.


Odala akapolowo amene mbuye wao, pakudza iye, adzawapeza odikira; indetu ndinena ndinu, kuti iye adzadzimangira m'chuuno, nadzawakhalitsa pansi kudya, nadzafika, nadzawatumikira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa