Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Nehemiya 7:63 - Buku Lopatulika

63 Ndi a ansembe: ana a Hobaya, ana a Hakozi, ana a Barizilai, amene anadzitengera mkazi wa ana aakazi a Barizilai Mgiliyadi, natchedwa ndi dzina lao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

63 Ndi a ansembe: ana a Hobaya, ana a Hakozi, ana a Barizilai, amene anadzitengera mkazi wa ana akazi a Barizilai Mgiliyadi, natchedwa ndi dzina lao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

63 Ndiponso ena mwa ansembe anali aŵa: a banja la Hobaya, a banja la Hakozi, a banja la Barizilai (kunena amene adaakwatira mmodzi mwa ana aakazi a Barizilai wa ku Giliyadi, nkutenga dzina la bambo waoyo).

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

63 Ndiponso ena pakati pa ansembe anali awa: zidzukulu za Hobiya, zidzukulu za Hakozi ndi zidzukulu za Barizilai (munthu amene anakwatira mwana wamkazi wa Barizilai wa ku Giliyadi ndipo amatchedwa dzina limenelo).

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 7:63
8 Mawu Ofanana  

Ndipo kunali pakufika Davide ku Mahanaimu, Sobi mwana wa Nahasi wa ku Raba wa ana a Amoni, ndi Makiri mwana wa Amiyele wa ku Lodebara, ndi Barizilai Mgiliyadi wa ku Rogelimu,


Koma uchitire zokoma ana aamuna aja a Barizilai wa ku Giliyadi, akhale pakati pa akudyera pa gome lako, popeza momwemo amenewo anandiyandikira muja ndinalikuthawa Abisalomu mbale wako.


Ndipo Hakozi anabala Anubu, ndi Zobeba, ndi mabanja a Ahariyele mwana wa Harumu.


Ndi pambali pao anakonza Meremoti mwana wa Uriya, mwana wa Hakozi. Ndi pambali pao anakonza Mesulamu mwana wa Berekiya, mwana wa Mesezabele. Ndi pambali pao anakonza Zadoki mwana wa Baana.


ana a Delaya, ana a Tobiya, ana a Nekoda, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi anai kudza awiri.


Awa anafunafuna maina ao m'buku la iwo owerengedwa mwa chibadwidwe, koma osawapeza; potero anawayesa odetsedwa, nawachotsa kuntchito ya nsembe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa