Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




2 Samueli 18:4 - Buku Lopatulika

Ndipo mfumu inanena nao, Ndidzachita chimene chikomera inu. Mfumu inaima pambali pa chipata, ndipo anthu onse anatuluka ali mazana, ndi zikwi.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo mfumu inanena nao, Ndidzachita chimene chikomera inu. Mfumu niima pambali pa chipata, ndipo anthu onse anatuluka ali mazana, ndi zikwi.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mfumu idaŵauza kuti, “Chilichonse chimene chikukomereni, ndidzachita.” Choncho mfumuyo idakaimirira pambali pa chipata nthaŵi imene gulu lonse lankhondo linkatuluka mazanamazana, ndiponso zikwizikwi.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mfumu inayankha kuti, “Ine ndichita chimene chili chokukomerani.” Kotero mfumu inayima pambali pa chipata pamene ankhondo onse amayenda mʼmagulu a anthu 100 ndi a 1,000.

Onani mutuwo



2 Samueli 18:4
5 Mawu Ofanana  

Ndipo Davide anawerenga anthu amene anali naye, nawaikira atsogoleri a zikwi ndi atsogoleri a mazana.


Koma Davide anakhala pakati pa zipata ziwiri; ndipo mlonda anakwera pa tsindwi la chipata cha kulinga, natukula maso ake, napenya; naona munthu alikuthamanga yekha.


Ndipo mfumu inalamulira Yowabu ndi Abisai ndi Itai, kuti, Chifukwa cha ine muchite mofatsa ndi mnyamatayo, Abisalomu. Ndipo anthu onse anamva pamene mfumu inalamulira atsogoleriwo za Abisalomu.


ndipo adzakhala mzimu wa chiweruziro kwa oweruza milandu, ndi mphamvu kwa iwo amene abweza nkhondo pachipata.


Ndipo akalonga a Afilisti ananyamuka ndi mazana ao ndi zikwi zao; ndipo Davide ndi anthu ake ananyamuka ndi a pambuyo pamodzi ndi Akisi.