Koma Abisalomu anathawa. Ndipo mnyamata wakudikira anatukula maso ake nayang'ana, ndipo onani, m'mbuyo mwake anthu ambiri analikubwera m'njira yolambalala phiri.
2 Samueli 18:24 - Buku Lopatulika Koma Davide anakhala pakati pa zipata ziwiri; ndipo mlonda anakwera pa tsindwi la chipata cha kulinga, natukula maso ake, napenya; naona munthu alikuthamanga yekha. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Davide anakhala pakati pa zipata ziwiri; ndipo mlonda anakwera pa tsindwi la chipata cha kulinga, natukula maso ake, napenya; naona munthu alikuthamanga yekha. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nthaŵi imeneyo nkuti Davide atakhala pakati pa zipata ziŵiri, chakubwalo ndi cham'kati. Mlonda adakwera pa khoma nakaimirira pa denga la chipata. Adati atayang'ana, adaona munthu akuthamanga yekhayekha. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nthawi imeneyo nʼkuti Davide atakhala pakati pa zipata ziwiri, chakubwalo ndi chamʼkati. Mlonda anakwera pa khoma nakayimirira pa denga la chipata. Anati atayangʼana, anaona munthu akuthamanga yekhayekha. |
Koma Abisalomu anathawa. Ndipo mnyamata wakudikira anatukula maso ake nayang'ana, ndipo onani, m'mbuyo mwake anthu ambiri analikubwera m'njira yolambalala phiri.
Koma ngakhale kotero, anati iye, Ndithamange. Iye nanena naye, Thamanga. Ndipo Ahimaazi anathamanga njira ya kuchigwa, napitirira Mkusi.
Pamenepo mlondayo anafuula, nauza mfumu. Mfumuyo niti, Ngati ali yekha alikubwera ndi mau. Ndipo iye uja anayenda msanga, nayandikira.
Ndipo mfumu inanena nao, Ndidzachita chimene chikomera inu. Mfumu inaima pambali pa chipata, ndipo anthu onse anatuluka ali mazana, ndi zikwi.
Pamenepo mfumu inanyamuka, nikakhala pachipata. Ndipo anauza anthu kuti, Onani mfumu ilikukhala pachipata; anthu onse nadza pamaso pa mfumu. Koma Aisraele adathawa, munthu yense ku hema wake.
Pakufika iye, onani, Eli analikukhala pampando m'mbali mwa njira, alikuyang'anira, popeza mtima wake unanthunthumira chifukwa cha likasa la Mulungu. Pamene munthu uja anafika m'mzindamo, nanena izi, a m'mzinda monse analira.