Ndipo Yowabu ananena ndi womuuzayo, Ndipo taona, unamuona, tsono unalekeranji kumkantha agwe pansi pomwepo? Ndipo ine ndikadakupatsa ndalama khumi ndi lamba.
2 Samueli 18:12 - Buku Lopatulika Munthuyo nanena ndi Yowabu, Ndingakhale ndikalandira ndalama chikwi m'dzanja langa, koma sindikadasamula dzanja langa pa mwana wa mfumu; pakuti m'kumva kwathu mfumu inalamulira inu ndi Abisai ndi Itai, kuti, Chenjerani munthu yense asakhudze mnyamatayo Abisalomu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Munthuyo nanena ndi Yowabu, Ndingakhale ndikalandira ndalama chikwi m'dzanja langa, koma sindikadasamula dzanja langa pa mwana wa mfumu; pakuti m'kumva kwathu mfumu inalamulira inu ndi Abisai ndi Itai, kuti, Chenjerani munthu yense asakhudze mnyamatayo Abisalomu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma munthuyo adauza Yowabu kuti, “Ngakhale ndikadalandira m'manja mwangamu ndalama zasiliva zokwanira 1,000, sindikadasamula dzanja langa kuti ndiphe mwana wa mfumu. Paja mfumu idakulamulani inu ndi Abisai ndi Itai, ife tilikumva, kuti, ‘Mumtchinjirize mwanayo Abisalomu chifukwa cha ine.’ Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma munthuyo anayankha kuti, “Ngakhale atandipatsa mʼmanja mwanga ndalama zasiliva 1,000, sindingatambasule dzanja langa kupha mwana wa mfumu. Ife tikumva, mfumu inalamula inu Abisai ndiponso Itai kuti, ‘Mutetezeni mnyamatayo Abisalomu chifukwa cha ine!’ |
Ndipo Yowabu ananena ndi womuuzayo, Ndipo taona, unamuona, tsono unalekeranji kumkantha agwe pansi pomwepo? Ndipo ine ndikadakupatsa ndalama khumi ndi lamba.
Ndipo mfumu inalamulira Yowabu ndi Abisai ndi Itai, kuti, Chifukwa cha ine muchite mofatsa ndi mnyamatayo, Abisalomu. Ndipo anthu onse anamva pamene mfumu inalamulira atsogoleriwo za Abisalomu.