Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




2 Samueli 16:19 - Buku Lopatulika

Ndiponso ndidzatumikira yani? Si pamaso pa mwana wake nanga? Monga ndinatumikira pamaso pa atate wanu, momwemo ndidzakhala pamaso panu.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndiponso ndidzatumikira yani? Si pamaso pa mwana wake nanga? Monga ndinatumikira pamaso pa atate wanu, momwemo ndidzakhala pamaso panu.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Nanganso ndani amene ine ndingamtumikire? Kodi si inuyo mwana wa mfumu? Monga momwe ndidatumikira bambo wanu, momwemonso ndidzakutumikirani inu.”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Kodi ndidzatumikiranso yani? Kodi sinditumikira mwana wa mfumu? Monga momwe ndinatumikira abambo anu, kotero ndidzatumikiranso inu.”

Onani mutuwo



2 Samueli 16:19
7 Mawu Ofanana  

koma ukabwerera kumzinda, ndi kunena ndi Abisalomu, Ine ndine mnyamata wanu, mfumu; monga kale ndinali mnyamata wa atate wanu, momwemo tsopano ndidzakhala mnyamata wanu; pomwepo udzanditsutsira uphungu wa Ahitofele.


Husai nanena ndi Abisalomu, Iai; koma amene Yehova anasankha ndi anthu awa, ndi anthu onse a Israele, ine ndili wake, ndipo ndidzakhala naye iyeyu.


Pomwepo Abisalomu ananena ndi Ahitofele, Upangire chimene ukuti tikachite.


Pakamwa pake mposalala ngati mafuta amkaka, koma mumtima mwake munali nkhondo, mau ake ngofewa ngati mafuta oyenga, koma anali malupanga osololasolola.


Ndipo Ayuda otsala anawagwiranso m'maso pamodzi naye; kotero kuti Barnabasinso anatengedwa ndi kugwira m'maso kwao.


Ndipo Davide anati kwa Akisi, Potero mudzadziwe chimene mnyamata wanu adzachita. Ndipo Akisi anati kwa Davide, Chifukwa chake ndidzakuika iwe ukhale wondisungira moyo wanga masiku onse.


Ndipo Davide ananena ndi Akisi, Koma ndinachitanji? Ndipo munapeza chiyani mwa mnyamata wanu nthawi yonse ndili pamaso panu kufikira lero, kuti sindingapite kukaponyana nkhondo ndi adani a mbuye wanga mfumu?