1 Samueli 29:8 - Buku Lopatulika8 Ndipo Davide ananena ndi Akisi, Koma ndinachitanji? Ndipo munapeza chiyani mwa mnyamata wanu nthawi yonse ndili pamaso panu kufikira lero, kuti sindingapite kukaponyana nkhondo ndi adani a mbuye wanga mfumu? Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20148 Ndipo Davide ananena ndi Akisi, Koma ndinachitanji? Ndipo munapeza chiyani mu mnyamata wanu nthawi yonse ndili pamaso panu kufikira lero, kuti sindingapite kukaponyana nkhondo ndi adani a mbuye wanga mfumu? Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa8 Davide adamufunsa kuti, “Kodi ndachita chiyani? Kodi mwapeza chiyani pa ine mtumiki wanu, kuyambira nthaŵi imene ndidayamba kukugwirirani ntchito mpaka tsopano lino? Nanga ndilekerenji kukamenyana nkhondo ndi adani anu, mbuyanga mfumu?” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero8 Davide anafunsa Akisi kuti, “Kodi ndachita chiyani? Kodi mwapeza cholakwa chotani mwa ine mtumiki wanu chiyambire kukutumikirani mpaka lero? Tsono chifukwa chiyani sindingapite kukamenya nkhondo ndi adani a mbuye wanga mfumu?” Onani mutuwo |
Ndikalipo ine; chitani umboni wonditsutsa pamaso pa Yehova, ndi pamaso pa wodzozedwa wake; ndinalanda ng'ombe ya yani? Kapena ndinalanda bulu wa yani? Ndinanyenga yani? Ndinasutsa yani? Ndinalandira m'manja mwa yani chokometsera mlandu kutseka nacho maso anga? Ngati ndinatero ndidzachibwezera kwa inu.