Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 15:34 - Buku Lopatulika

34 koma ukabwerera kumzinda, ndi kunena ndi Abisalomu, Ine ndine mnyamata wanu, mfumu; monga kale ndinali mnyamata wa atate wanu, momwemo tsopano ndidzakhala mnyamata wanu; pomwepo udzanditsutsira uphungu wa Ahitofele.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

34 koma ukabwerera kumudzi, ndi kunena ndi Abisalomu, Ine ndine mnyamata wanu, mfumu; monga kale ndinali mnyamata wa atate wanu, momwemo tsopano ndidzakhala mnyamata wanu; pomwepo udzanditsutsira uphungu wa Ahitofele.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

34 Koma makamaka iwe ubwerere ku mzinda, ukamuuze Abisalomu kuti, ‘Inu amfumu, ine ndidzakhala mtumiki wanu. Monga kale ndinali mtumiki wa bambo wanu, momwemonso tsopano ndidzakhala mtumiki wanu.’ Ukakatero ukandigonjetsera uphungu wa Ahitofele.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

34 Koma ngati ubwerera ku mzinda ndi kukanena kwa Abisalomu kuti, ‘Inu mfumu ine ndidzakhala wantchito wanu.’ Mʼmbuyomu ndinali wantchito wa abambo anu koma tsopano ndidzakhala wantchito wanu. Ukatero udzandithandiza kulepheretsa malangizo a Ahitofele.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 15:34
5 Mawu Ofanana  

Popeza unangofika dzulo lokha, kodi ndidzakutenga lero kuyendayenda nafe popeza ndipita pomwe ndiona popita? Ubwerere nubwereretsenso abale ako; chifundo ndi zoonadi zikhale nawe.


Taonani, Ine ndikutumizani inu monga nkhosa pakati pa mimbulu; chifukwa chake khalani ochenjera monga njoka, ndi oona mtima monga nkhunda.


ndipo uzimchitira Ai ndi mfumu yake monga umo unamchitira Yeriko ndi mfumu yake; koma zofunkha zake ndi ng'ombe zake mudzifunkhire nokha; udziikire anthu alalire kukhonde kwa mzinda.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa