Atero Yehova, Taona ndidzakuutsira zoipa, zobadwa m'nyumba yako ya iwe wekha; ndipo ndidzachotsa akazi ako pamaso pako ndi kuwapatsa mnansi wako, amene adzagona ndi akazi ako dzuwa lili denene.
2 Samueli 15:1 - Buku Lopatulika Ndipo kunali, chitapita ichi Abisalomu anadzikonzera galeta ndi akavalo ndi anthu makumi asanu akuthamanga momtsogolera. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo kunali, chitapita ichi Abisalomu anadzikonzera galeta ndi akavalo ndi anthu makumi asanu akuthamanga momtsogolera. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Zitapita zimenezi, Abisalomu adadzipezera galeta lokokedwa ndi akavalo, napezanso anthu makumi asanu omamperekeza. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Patapita nthawi, Abisalomu anadzipezera galeta ndi akavalo pamodzi ndi amuna makumi asanu amene amathamanga patsogolo pake. |
Atero Yehova, Taona ndidzakuutsira zoipa, zobadwa m'nyumba yako ya iwe wekha; ndipo ndidzachotsa akazi ako pamaso pako ndi kuwapatsa mnansi wako, amene adzagona ndi akazi ako dzuwa lili denene.
Ndipo mfumu inati kwa iwo, Tengani akapolo a mfumu yanu, nimukweze Solomoni mwana wanga pa nyuru yangayanga, nimutsikire naye ku Gihoni.
Pamenepo Adoniya mwana wa Hagiti anadzikuza, nati, Ndikhala mfumu ndine; nadzikonzera agaleta ndi apakavalo ndi anthu makumi asanu omtsogolera mothamanga.
Ena atama magaleta, ndi ena akavalo; koma ife tidzatchula dzina la Yehova Mulungu wathu.
Koma asadzichulukitsire akavalo iye, kapena kubwereretsa anthu anke ku Ejipito, kuti achulukitse akavalo; popeza Yehova anati nanu, Musamabwereranso njira iyi.
Nati, Awa ndi makhalidwe a mfumu imene idzaweruza inu; idzatenga ana anu aamuna, akhale akusunga magaleta, ndi akavalo ake; ndipo adzathamanga ndi kutsogolera magaleta ake;