Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mafumu 1:5 - Buku Lopatulika

5 Pamenepo Adoniya mwana wa Hagiti anadzikuza, nati, Ndikhala mfumu ndine; nadzikonzera agaleta ndi apakavalo ndi anthu makumi asanu omtsogolera mothamanga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Pamenepo Adoniya mwana wa Hagiti anadzikuza, nati, Ndikhala mfumu ndine; nadzikonzera agaleta ndi apakavalo ndi anthu makumi asanu omtsogolera mothamanga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Tsono Adoniya, mwana wa Hagiti, adayamba kudzikuza namanena kuti, “Ndidzakhala mfumu ndine.” Motero adadzipezera magaleta ndi anthu okwera pa akavalo, ndiponso anthu operekeza makumi asanu oti azithamanga patsogolo pake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Nthawi imeneyi Adoniya, mwana wa Hagiti, anayamba kudzitukumula ndipo anati, “Ndidzakhala mfumu ndine.” Choncho anadzikonzera galeta ndi akavalo, pamodzi ndi anthu 50 woti azithamanga patsogolo pake.

Onani mutuwo Koperani




1 Mafumu 1:5
19 Mawu Ofanana  

Ndipo kunali, chitapita ichi Abisalomu anadzikonzera galeta ndi akavalo ndi anthu makumi asanu akuthamanga momtsogolera.


ndi wachinai Adoniya mwana wa Hagiti; ndi wachisanu Sefatiya mwana wa Abitala;


Pamenepo Natani ananena ndi Bateseba amake wa Solomoni, nati, Kodi sunamve kuti Adoniya mwana wa Hagiti walowa ufumu, ndipo Davide mbuye wathu sadziwa?


Ndipo namwaliyo anali wokongola ndithu, namasunga mfumu namtumikira; koma mfumu sinamdziwe.


Pomwepo Adoniya mwana wa Hagiti anadza kwa Bateseba amai wake wa Solomoni, ndipo mkaziyo anati, Kodi wadza ndi mtendere? Nati, Ndi mtendere umene.


Nati iye, Mudziwa kuti ufumu unali wanga, ndi kuti Aisraele onse anaika maso ao pa ine, kuti ndikhale mfumu ndine; koma ufumu watembenuka nukhala wa mbale wanga, popeza iye anaulandira kwa Yehova.


Ndipo tsono, pali Yehova amene wandikhazikitsa ine, nandikhalitsa pampando wachifumu wa Davide atate wanga, nandimangira nyumba monga analonjeza, zedi Adoniya aphedwa lero lomwe.


ndi mwa ana anga onse (pakuti Yehova wandipatsa ana aamuna ambiri), anasankha Solomoni mwana wanga akhale pa mpando wachifumu wa ufumu wa Yehova kuweruza Israele.


Mfumu Davide ananenanso kwa khamu lonse, Mulungu wasankha mwana wanga Solomoni yekha, ndiye mnyamata ndi wosakhwima; ndipo ntchitoyi ndi yaikulu, pakuti chinyumbachi sichili cha munthu, koma cha Yehova Mulungu.


wachitatu Abisalomu mwana wa Maaka mwana wamkazi wa Talimai mfumu ya Gesuri, wachinai Adoniya mwana wa Hagiti,


Kodi udzikwezanso pa anthu anga, ndi kusawalola amuke?


Kunyada kutsogolera kuonongeka; mtima wodzikuza ndi kutsogolera kuphunthwa.


Mtima wa munthu unyada asanaonongeke; koma chifatso chitsogolera ulemu.


Dziko lao ladzala siliva ndi golide, ngakhale chuma chao nchosawerengeka; dziko lao lidzalanso akavalo, ngakhale magaleta ao ngosawerengeka.


Chifukwa munthu aliyense wakudzikuza adzachepetsedwa; ndipo wakudzichepetsa adzakulitsidwa.


Ndinena ndi inu, anatsikira kunyumba kwake woyesedwa wolungama uyutu, wosati uja ai; pakuti yense wakudzikuza yekha adzachepetsedwa; koma wodzichepetsa yekha adzakulitsidwa.


Nenanitu m'makutu mwa eni ake onse a ku Sekemu, Chokomera inu nchiti, akulamulireni ana aamuna onse a Yerubaala ndiwo amuna makumi asanu ndi awiri, kapena akulamulireni mwamuna mmodzi? Mukumbukirenso kuti ine ndine wa fuko lanu ndi nyama yanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa