Ndipo ndinawatumiza kwa Ido mkulu, kumalo dzina lake Kasifiya; ndinalonganso m'kamwa mwao mau akunena kwa Ido, ndi kwa abale ake antchito a m'kachisi, pamalo paja Kasifiya, kuti azibwera nao kwa ife otumikira za nyumba ya Mulungu wathu.
Ndipo ndaika mau anga m'kamwa mwako; ndipo ndakuphimba ndi mthunzi wa dzanja langa, kuti ndikhazike kumwamba ndi kuika maziko a dziko lapansi, ndi kunena kwa Ziyoni, Inu ndinu anthu anga.
Ndipo kunena za Ine, ili ndi pangano langa ndi iwo, ati Yehova; mzimu wanga umene uli pa iwe, ndi mau anga amene ndaika m'kamwa mwako sadzachoka m'kamwa mwako, pena m'kamwa mwa ana ako, pena m'kamwa mwa mbeu ya mbeu yako, ati Yehova, kuyambira tsopano ndi kunthawi zonse.