Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 14:2 - Buku Lopatulika

2 Ndipo Yowabu anatumiza ku Tekowa, natenga kumeneko mkazi wanzeru, nanena naye, Ukokomezeke monga mfedwa, nuvale zovala za pamaliro, osadzola mafuta, koma ukhale ngati munthu wamkazi wakulira akufa nthawi yaikulu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndipo Yowabu anatumiza ku Tekowa, natenga kumeneko mkazi wanzeru, nanena naye, Ukokomezeke monga mfedwa, nuvale zovala za pamaliro, osadzola mafuta, koma ukhale ngati munthu wamkazi wakulira akufa nthawi yaikulu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Tsono adatuma anthu ku Tekowa kukatengako mkazi wanzeru kumeneko. Adauza mkaziyo kuti, “Ukhale ngati mfedwa, uvale zovala zaumasiye. Usadzole mafuta, koma ukhale ngati mkazi amene wakhala akulira masiku ambiri.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Kotero Yowabu anatuma munthu wina kupita ku Tekowa ndi kukatengako mkazi wanzeru. Yowabu anati kwa mkaziyo, “Ukhale ngati namfedwa. Uvale zovala zaumasiye ndipo usadzole mafuta ena aliwonse. Ukhale ngati mkazi amene wakhala akulira masiku ambiri.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 14:2
17 Mawu Ofanana  

Ndipo mkazi anauka nachoka, navula chofunda chake, navala zovala zamasiye zake.


Ndipo pamene mkazi wa Uriya anamva kuti Uriya mwamuna wake adamwalira, iye analira maliro a mwamuna wake.


Pamenepo Davide ananyamuka pansi, nasamba, nadzola, nasintha zovala; nafika kunyumba ya Yehova, napembedza; pamenepo anafika kunyumba yake; ndipo powauza anamuikira chakudya, nadya iye.


Pamenepo mkazi wanzeru wa m'mzindamo anafuula, kuti, Imvani, imvani; munene kwa Yowabu, Bwerani pafupi kuno kuti ndilankhule nanu.


Helezi Mpaliti, Ira mwana wa Ikesi Mtekowa.


Ndipo Yerobowamu ananena ndi mkazi wake, Unyamuke, nudzizimbaitse, ungadziwike kuti ndiwe mkazi wa Yerobowamu, nupite ku Silo; taona, kumeneko kuli Ahiya mneneri uja anandiuza ine ndidzakhala mfumu ya anthu awa.


Ndipo Yehova ananena ndi Ahiya, Taona, mkazi wa Yerobowamu akudza kukufunsa za mwana wake, popeza adwala; udzanena naye mwakutimwakuti; popeza kudzakhala pakulowa iye adzadzizimbaitsa.


Anamangadi Betelehemu, ndi Etamu, ndi Tekowa,


Nalawira mamawa, natuluka kunka kuchipululu cha Tekowa; ndipo potuluka iwo, Yehosafati anakhala chilili, nati, Mundimvere ine, Ayuda inu, ndi inu okhala mu Yerusalemu, limbikani mwa Yehova Mulungu wanu, ndipo mudzakhazikika; khulupirirani aneneri ake, ndipo mudzalemerera.


Potsatizana nao Atekowa anakonza gawo lina, pandunji pa nsanja yaikulu yosomphoka ndi kulinga la Ofele.


Ndi pambali pao anakonza Atekowa; koma omveka ao sanapereke makosi ao kuntchito ya Mbuye wao.


ndi vinyo wokondweretsa mtima wa munthu, ndi mafuta akunyezimiritsa nkhope yake, ndi mkate wakulimbitsa mtima wa munthu.


Zovala zako zikhale zoyera masiku onse; mutu wako usasowe mafuta.


Ananu a Benjamini, pulumukani pothawa pakati pa Yerusalemu, ombani lipenga mu Tekowa, kwezani chizindikiro mu Betehakeremu; pakuti chaoneka choipa chotuluka m'mpoto ndi kuononga kwakukulu.


Mau a Amosi, amene anali mwa oweta ng'ombe a ku Tekowa, ndiwo amene anawaona za Israele masiku a Uziya mfumu ya Yuda, ndi masiku a Yerobowamu mwana wa Yowasi mfumu ya Israele, zitatsala zaka ziwiri chisanafike chivomezi.


Koma iwe, posala kudya, dzola mutu wako, ndi kusamba nkhope yako:


Usambe tsono, nudzole, nuvale zovala zako, nutsikire popunthirapo, koma usadziwike naye munthuyo, koma atatha kudya ndi kumwa ndiko.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa