Ndipo kunali pa madzulo Davide anauka pa kama wake nayenda pa tsindwi la nyumba ya mfumu. Ndipo iye ali patsindwipo anaona mkazi alinkusamba; ndi mkaziyo anali wochititsa kaso pomuyang'ana.
2 Samueli 14:27 - Buku Lopatulika Ndipo kwa Abisalomu kunabadwa ana aamuna atatu ndi mwana wamkazi mmodzi, dzina lake ndiye Tamara, iye ndiye mkazi wokongola nkhope. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo kwa Abisalomu kunabadwa ana amuna atatu ndi mwana wamkazi mmodzi, dzina lake ndiye Tamara, iye ndiye mkazi wokongola nkhope. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Abisalomu anali ndi ana aamuna atatu, ndi mwana wamkazi mmodzi, dzina lake Tamara. Iyeyu anali mkazi wokongola. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Abisalomu anali ndi ana aamuna atatu ndi wamkazi mmodzi. Mwana wamkazi dzina lake linali Tamara, ndipo anali mkazi wokongola kwambiri. |
Ndipo kunali pa madzulo Davide anauka pa kama wake nayenda pa tsindwi la nyumba ya mfumu. Ndipo iye ali patsindwipo anaona mkazi alinkusamba; ndi mkaziyo anali wochititsa kaso pomuyang'ana.
Ndipo kunali chitapita ichi, popeza Abisalomu mwana wa Davide anali naye mlongo wake wokongola, dzina lake ndiye Tamara, Aminoni mwana wa Davide anamkonda iye.
Koma Abisalomu akali moyo adatenga nadziutsira choimiritsacho chili m'chigwa cha mfumu; pakuti anati, Ndilibe mwana wamwamuna adzakhala chikumbutso cha dzina langa; natcha choimiritsacho ndi dzina la iye yekha; ndipo chitchedwa chikumbutso cha Abisalomu, kufikira lero lomwe.
Ndipo Ine ndidzawaukira, ati Yehova wa makamu, ndi kuononga ku Babiloni dzina ndi otsala, ndi mwana wamwamuna, ndi chidzukulu chachimuna, ati Yehova.
Atero Yehova, Lembani munthu uyu wopanda ana, munthu wosaona phindu masiku ake; pakuti palibe munthu wa mbeu zake adzaona phindu, ndi kukhala pa mpando wachifumu wa Davide, ndi kulamuliranso mu Yuda.