Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 22:30 - Buku Lopatulika

30 Atero Yehova, Lembani munthu uyu wopanda ana, munthu wosaona phindu masiku ake; pakuti palibe munthu wa mbeu zake adzaona phindu, ndi kukhala pa mpando wachifumu wa Davide, ndi kulamuliranso mu Yuda.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

30 Atero Yehova, Lembani munthu uyu wopanda ana, munthu wosaona phindu masiku ake; pakuti palibe munthu wa mbeu zake adzaona phindu, ndi kukhala pa mpando wachifumu wa Davide, ndi kulamuliranso m'Yuda.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

30 Chauta akuti, “Munthu ameneyu mumtenge ngati wopanda ana, munthu amene sadzakhoza pa moyo wake. Ndithu, palibe ndi mmodzi yemwe mwa zidzukulu zake amene adzakhale pa mpando waufumu wa Davide ndi kudzalamuliranso Yuda.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

30 Yehova akuti, “Munthu ameneyu mumutenge ngati wopanda ana, munthu amene sadzakhala wochita bwino pamoyo wake wonse, pakuti palibe ndi mmodzi yemwe mwa zidzukulu zake zomwe zidzachita bwino. Palibe amene adzathe kukhala pa mpando waufumu wa Davide ndi kulamulira Yuda.”

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 22:30
11 Mawu Ofanana  

Sadzakhala naye mwana kapena chidzukulu mwa anthu a mtundu wake, kapena wina wotsalira kumene anakhalako.


Kodi uyenera kuyanjana ndi Inu mpando wachifumu wa kusakaza, wakupanga chovuta chikhale lamulo?


Pakuti abusa apulukira, sanafunsire kwa Yehova; chifukwa chake sanapindule; zoweta zao zonse zabalalika.


Koma udzatuluka kwa iyenso, manja ako pamutu pako; pakuti Yehova wakana zokhulupirira zako, ndipo sudzapindula m'menemo.


ndi kuti, Tamvani mau a Yehova, Inu mfumu ya Yuda, amene mukhala pa mpando wa Davide, inu, ndi atumiki anu, ndi anthu anu amene alowa pa zipata izi.


chifukwa chake atero Yehova, Taonani, ndidzalanga Semaya Mnehelamu, ndi mbeu zake; sadzakhala ndi munthu wakukhala mwa anthu awa, sadzaona zabwino ndidzachitira anthu anga, ati Yehova: chifukwa wanena zopikisana ndi Yehova.


Chifukwa chake Yehova atero za Yehoyakimu mfumu ya Yuda: Adzasowa wokhala pa mpando wachifumu wa Davide; ndipo mtembo wake udzaponyedwa usana kunja kuli dzuwa, ndi usiku kuli chisanu.


Ndipo mfumu ya ku Babiloni inapha ana a Zedekiya pamaso pake; niphanso akulu onse a Yuda mu Ribula.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa