Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




2 Samueli 13:13 - Buku Lopatulika

Ndipo ine, manyazi anga ndidzapita nao kuti? Ndipo iwenso udzakhala ngati wina wa zitsiru mu Israele. Chifukwa chake tsono ulankhule ndi mfumu; iyeyu sadzakukaniza ine.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo ine, manyazi anga ndidzapita nao kuti? Ndipo iwenso udzakhala ngati wina wa zitsiru m'Israele. Chifukwa chake tsono ulankhule ndi mfumu; iyeyu sadzakukaniza ine.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Kodi ine sindidzachita manyazi poyenda pakati pa anthu? Ndipo iwe udzakhala mmodzi mwa zitsiru pakati pa Aisraele. Nchifukwa chake tsono, chonde, ndapota nawe, ulankhule ndi amfumu, poti iwowo sadzandikaniza kuti ndikwatiwe nawe.”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Kodi ukuganiza bwanji za ine? Kodi manyazi anga ndidzawachotsa bwanji? Ndipo nanga iweyo? Udzakhalatu monga mmodzi mwa zitsiru zoyipitsitsa muno mu Israeli. Chonde kapemphe kwa mfumu. Sadzakuletsa kuti undikwatire.”

Onani mutuwo



2 Samueli 13:13
4 Mawu Ofanana  

Taonanitu, ndili ndi ana aakazi awiri, amene sanadziwe mwamuna; ndiwatulutsire iwo kwa inu, muchite nao chomwe chikomera inu; koma anthu awa musawachitire iwo kanthu; chifukwa kuti anadza iwo pansi pa mthunzi wa tsindwi langa.


Koma ndiye mlongo wanga ndithu, mwana wa atate wanga, koma si mwana wa amai wanga: ndipo anakhala ndi ine mkazi wanga.


pamenepo azimtulutsa namwaliyo ku khomo la nyumba ya atate wake, ndipo amuna a mzinda wake azimponya miyala kuti afe; popeza anachita chopusa mu Israele, kuchita chigololo m'nyumba ya atate wake; chotero uzichotsa choipacho pakati panu.


Taonani, mwana wanga wamkazi ndiye namwali, ndi mkazi wake wamng'ono siwa; ndiwatulutse iwo, muwachepetse iwo, ndi kuwachitira monga muyesa chokoma; koma mwamuna uyu musamchitire chopusa ichi.