Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 13:14 - Buku Lopatulika

14 Koma iye sadafune kumvera mau ake, ndipo popeza anali wamphamvu ndi iye, anamkakamiza, nagona naye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Koma iye sadafuna kumvera mau ake, ndipo popeza anali wamphamvu ndi iye, anamkakamiza, nagona naye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Koma Aminoni sadamve zimene ankanena Tamarazo. Ndipo popeza kuti anali ndi mphamvu zoposa Tamara, Aminoniyo adamkakamiza Tamarayo nagona naye.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Koma sanamvere zimene amanena Tamara ndipo popeza anali wamphamvu kuposa Tamarayo, iye anamugwirira.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 13:14
8 Mawu Ofanana  

Pamene anamuona iye Sekemu, mwana wake wamwamuna wa Hamori Muhivi, kalonga wa dzikolo, anamtenga nagona ndi iye, namuipitsa.


Atero Yehova, Taona ndidzakuutsira zoipa, zobadwa m'nyumba yako ya iwe wekha; ndipo ndidzachotsa akazi ako pamaso pako ndi kuwapatsa mnansi wako, amene adzagona ndi akazi ako dzuwa lili denene.


Atatero Aminoni anadana naye ndi chidani chachikulu kopambana; pakuti chidani chimene anamuda nacho, chinali chachikulu koposa chikondi adamkonda nacho. Ndipo Aminoni ananena naye, Nyamuka, choka.


Nibwera mfumu kumunda wa maluwa wa kuchinyumba kulowanso m'nyumba munali madyerero a vinyo, napeza Hamani atagwa pa kama wokhalapo Estere. Niti mfumu, Kodi aumiriza mkazi wamkulu pamaso panga m'nyumba? Potuluka mau pakamwa pa mfumu anamphimba Hamani nkhope.


Usamavula mlongo wako, mwana wamkazi wa atate wako, kapena mwana wamkazi wa mai wako, wobadwa kwanu, kapena wobadwa kwina.


Wotembereredwa iye wakugona ndi mlongo wake, mwana wamkazi wa atate wake, kapena mwana wamkazi wa make. Ndi anthu onse anene, Amen.


Nandiukira eni ake a Gibea, nandizingira nyumba usiku; nafuna kundipha ine, namchitira choipa mkazi wanga wamng'ono, nafa iye.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa