Saulo ndi Yonatani anali okoma ndi okondweretsa m'miyoyo yao, ndipo mu imfa yao sanasiyane; anali nalo liwiro loposa chiombankhanga, anali amphamvu koposa mikango.
2 Samueli 1:24 - Buku Lopatulika Ana aakazi inu a Israele, mulirire Saulo, amene anakuvekani ndi zofiira zokometsetsa, amene anaika zokometsetsa zagolide pa zovala zanu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ana akazi inu a Israele, mulirire Saulo, amene anakuvekani ndi zofiira zokometsetsa, amene anaika zokometsetsa zagolide pa zovala zanu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Inu akazi a ku Israele, mlireni Saulo. Chifukwa cha iye uja munkavala zovala zabwino zofiira, ndiponso munkaika zokometsera zagolide pa zovala zanu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Inu ana aakazi a Israeli, mulireni Sauli, amene anakuvekani zovala zofiira ndi zofewa, amene anakometsera zovala zanu ndi zokometsera zagolide. |
Saulo ndi Yonatani anali okoma ndi okondweretsa m'miyoyo yao, ndipo mu imfa yao sanasiyane; anali nalo liwiro loposa chiombankhanga, anali amphamvu koposa mikango.
Monga mphete yagolide ndi chipini chagolide woyengeka, momwemo wanzeru wodzudzula pa khutu lomvera.
Kodi angathe namwali kuiwala zokometsera zake, kapena mkwatibwi zovala zake? Koma anthu anga andiiwala Ine masiku osawerengeka.
Kodi sanapeze, sanagawe zofunkha? Namwali, anamwali awiri kwa munthu aliyense. Chofunkha cha nsalu za mawangamawanga kwa Sisera; chofunkha cha nsalu za mawangamawanga, za maluwa, nsalu za mawangamawanga, za maluwa konsekonse, kwa chofunkha cha khosi lake.