Ndipo pamene anthu okhala m'dzikomo, Akanani, anaona maliro a m'dwale la Atadi, anati, Awa ndi maliro aakulu a Aejipito: chifukwa chake dzina la pamenepo linatchedwa Abele-Mizraimu, pali tsidya lija la Yordani.
2 Samueli 1:17 - Buku Lopatulika Ndipo Davide analirira Saulo ndi Yonatani mwana wake ndi nyimbo iyi ya maliro; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Davide analirira Saulo ndi Yonatani mwana wake ndi nyimbo iyi ya maliro; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Choncho Davide adaimba nyimbo ya madandaulo, kulira Saulo ndi Yonatani mwana wake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Davide anayimba nyimbo iyi ya maliro, kulira Sauli ndi mwana wake Yonatani. |
Ndipo pamene anthu okhala m'dzikomo, Akanani, anaona maliro a m'dwale la Atadi, anati, Awa ndi maliro aakulu a Aejipito: chifukwa chake dzina la pamenepo linatchedwa Abele-Mizraimu, pali tsidya lija la Yordani.
Ndipo mfumu inanenera Abinere nyimbo iyi ya maliro, niti, Kodi Abinere anayenera kufa ngati chitsiru?
Ndipo Yeremiya anamlembera Yosiya nyimbo yomlira; ndi oimbira onse, amuna ndi akazi, amanena za Yosiya nyimbo za maliro zao mpaka lero lino; naziika zikhale lemba mu Israele; taonani, zilembedwa mu Nyimbo za Maliro.
Ndakhala ine monga ngati iye anali bwenzi langa, kapena mbale wanga; polira ndinaweramira pansi, monga munthu wakulira maliro amai wake.
Iyi ndi nyimbo ya maliro adzalira nayo, ana aakazi a amitundu adzachita nayo maliro; adzalirira nayo Ejipito ndi aunyinji ake onse, ati Ambuye Yehova.