Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




2 Akorinto 9:3 - Buku Lopatulika

Koma ndatuma abale kuti kudzitamandira kwathu kwa pa inu kusakhale kopanda pake m'menemo; kuti, monga ndinanena, mukakhale okonzekeratu;

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Koma ndatuma abale kuti kudzitamandira kwathu kwa pa inu kusakhale kopanda pake m'menemo; kuti, monga ndinanena, mukakhale okonzekeratu;

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Koma ndikutuma abale athuŵa, kuti kukunyadirani kwathu pa zimenezi kusakhale kwachabe, koma kuti mukhaledi okonzeka monga momwe ndidaanenera.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Koma ndikutumiza abalewo kuti kukunyadirani kwathu pa zimenezi kutsimikizike kuti si kwachabe ndi kuti mukhale okonzeka monga ndinanenera.

Onani mutuwo



2 Akorinto 9:3
7 Mawu Ofanana  

Pakuti ngati ndadzitamandira nako kanthu kwa iye chifukwa cha inu, sindinamvetsedwe manyazi; koma monga tinalankhula zonse ndi inu m'choonadi, koteronso kudzitamandira kwathu kumene kwa Tito, kunakhala choonadi.


Ndilimbika mtima kwambiri pakunena nanu, kudzitamandira kwanga chifukwa cha inu nkwakukulu; ndidzazidwa nacho chitonthozo, ndisefukira nacho chimwemwe m'chisautso chathu chonse.


Kotero kuti tinadandaulira Tito, kuti monga anayamba kale, chomwechonso atsirize kwa inu chisomo ichinso.


Uwakumbutse iwo agonje kwa akulu, ndi aulamuliro, akhale omvera, okonzeka pa ntchito iliyonse yabwino;