Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Akorinto 9:2 - Buku Lopatulika

2 pakuti ndidziwa chivomerezo chanu chimene ndidzitamandira nacho chifukwa cha inu ndi Amasedoniya, kuti Akaya anakonzekeratu chitapita chaka; ndi changu chanu chinautsa ochulukawo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 pakuti ndidziwa chivomerezo chanu chimene ndidzitamandira nacho chifukwa cha inu ndi Amasedoniya, kuti Akaya anakonzekeratu chitapita chaka; ndi changu chanu chinautsa ochulukawo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Ndikudziŵa kuti mumafunadi kuthandiza, ndipo ndimakunyadirani kwa anthu a ku Masedoniya chifukwa cha chimenechi. Ndimaŵauza kuti, “Abale a ku Akaiya adakonzeka kale chaka chatha kuti athandize.” Ndipo changu chanu chautsa ena ambiri.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Popeza ndikudziwa mtima wanu wofuna kuthandiza, ndipo ndakhala ndikuwawuza monyadira a ku Makedoniya za chimenechi. Ndimawawuza kuti inu a ku Akaya munakonzeka kale chaka chatha kuti mupereke. Ndipo changu chanu chapatsa chidwi ambiri mwa iwo kuti nawonso achitepo kanthu.

Onani mutuwo Koperani




2 Akorinto 9:2
14 Mawu Ofanana  

Tsono pamene Galio anali chiwanga cha Akaya, Ayuda ndi mtima umodzi anamuukira Paulo, nanka naye kumpando wachiweruziro,


Ndipo zitapita zaka zambiri ndinadza kutengera mtundu wanga zachifundo, ndi zopereka;


Pakuti kunakondweretsa a ku Masedoniya ndi Akaya kuchereza osauka a kwa oyera mtima a ku Yerusalemu.


Koma ndikupemphani inu, abale, (mudziwa banja la Stefanasi, kuti ali chipatso choyamba cha Akaya, ndi kuti anadziika okha kutumikira oyera mtima),


Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu, mwa chifuniro cha Mulungu, ndi Timoteo mbaleyo, kwa Mpingo wa Mulungu umene uli ku Korinto, pamodzi ndi oyera mtima onse amene ali mu Akaya monse:


Pakuti ngati ndadzitamandira nako kanthu kwa iye chifukwa cha inu, sindinamvetsedwe manyazi; koma monga tinalankhula zonse ndi inu m'choonadi, koteronso kudzitamandira kwathu kumene kwa Tito, kunakhala choonadi.


Ndilimbika mtima kwambiri pakunena nanu, kudzitamandira kwanga chifukwa cha inu nkwakukulu; ndidzazidwa nacho chitonthozo, ndisefukira nacho chimwemwe m'chisautso chathu chonse.


Ndipo m'menemo nditchula choyesa ine; pakuti chimene chipindulira inu, amene munayamba kale chaka chapitachi si kuchita kokha, komanso kufunira.


Koma tsopano tsirizani kuchitaku; kuti monga kunali chivomerezo cha kufunira, koteronso kukhale kutsiriza kwake m'chimene muli nacho.


ndipo si ichi chokha, komanso anasankhika ndi Mipingo, apite limodzi ndi ife m'chisomo ichi, chimene tichitumikira ife, kwa ulemerero wa Ambuye, ndi kuonetsa chivomerezo chathu;


Chifukwa chake muwatsimikizire iwo chitsimikizo cha chikondi chanu, ndi cha kudzitamandira kwathu pa inu pamaso pa Mipingo.


Sindinena ichi monga kulamulira, koma kuyesa mwa khama la ena choonadi cha chikondi chanunso.


kotero kuti munayamba kukhala inu chitsanzo kwa onse akukhulupirira mu Masedoniya ndi mu Akaya.


ndipo tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa