Pamenepo anaikanso manja m'maso mwake; ndipo anapenyetsa, nachiritsidwa, naona zonse mbee.
2 Akorinto 3:13 - Buku Lopatulika ndipo si monga Mose, amene anaika chophimba pa nkhope yake, kuti ana a Israele asayang'anitse pa chimaliziro cha chimene chinalikuchotsedwa; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndipo si monga Mose, amene anaika chophimba pa nkhope yake, kuti ana a Israele asayang'anitse pa chimaliziro cha chimene chinalikuchotsedwa; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Sitichita ngati Mose amene ankaphimba nkhope yake ndi nsalu, kuwopa kuti Aisraele angamapenye kutha kwake kwa kuŵala kosakhalitsa kuja. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ife sitili ngati Mose amene amaphimba nkhope yake kuopa kuti Aisraeli angaone kuti kunyezimira kwa nkhope yake kumazilala. |
Pamenepo anaikanso manja m'maso mwake; ndipo anapenyetsa, nachiritsidwa, naona zonse mbee.
Pakuti Khristu ali chimaliziro cha lamulo kulinga kuchilungamo kwa aliyense amene akhulupirira.
Koma ngati utumiki wa imfa wolembedwa ndi wolochedwa m'miyala, unakhala mu ulemerero, kotero kuti ana a Israele sanathe kuyang'anitsa pa nkhope yake ya Mose, chifukwa cha ulemerero wa nkhope yake, umene unalikuchotsedwa: