Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Marko 8:25 - Buku Lopatulika

25 Pamenepo anaikanso manja m'maso mwake; ndipo anapenyetsa, nachiritsidwa, naona zonse mbee.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

25 Pamenepo anaikanso manja m'maso mwake; ndipo anapenyetsa, nachiritsidwa, naona zonse mbee.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

25 Yesu adamuikanso manja kumaso kwake. Munthu uja adayang'anitsitsa ndipo adachira, nayamba kumapenya zonse bwino lomwe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

25 Kenakanso Yesu anayika manja ake mʼmaso a munthuyo. Ndipo maso ake anatsekuka, naonanso, ndipo anaona zonse bwinobwino.

Onani mutuwo Koperani




Marko 8:25
9 Mawu Ofanana  

Koma mayendedwe a olungama akunga kuunika kwa mbandakucha, kunkabe kuwala kufikira usana woti mbee.


Pakuti yense amene ali nazo, kudzapatsidwa kwa iye, ndimo adzakhala nazo zochuluka; koma yense amene alibe, chingakhale chomwe ali nacho chidzachotsedwa kwa iye.


Ndipo anakweza maso, nanena, Ndiona anthu; pakuti ndiwapenya ayendayenda ngati mitengo.


Ndipo anamtumiza amuke kwao, nanena, Usalowe konse m'mudzi.


Ndipo pakukhala iwo chipenyerere kumwamba pomuka Iye, taonani, amuna awiri ovala zoyera anaimirira pambali pao;


Ameneyo anamva Paulo alinkulankhula; ndipo Paulo pomyang'anitsa, ndi kuona kuti anali ndi chikhulupiriro cholandira nacho moyo,


pokhulupirira pamenepo, kuti Iye amene anayamba mwa inu ntchito yabwino, adzaitsiriza kufikira tsiku la Yesu Khristu;


Koma inu ndinu mbadwa yosankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mwini wake, kotero kuti mukalalikire zoposazo za Iye amene anakuitanani mutuluke mumdima, mulowe kuunika kwake kodabwitsa;


Koma kulani m'chisomo ndi chizindikiritso cha Ambuye wathu ndi Mpulumutsi Yesu Khristu; kwa Iye kukhale ulemerero, tsopano ndi nthawi zonse. Amen.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa