Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




2 Akorinto 2:16 - Buku Lopatulika

koma kwa ena fungo la moyo kumoyo. Ndipo azikwanira ndani izi?

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

koma kwa ena fungo la moyo kumoyo. Ndipo azikwanira ndani izi?

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Kwa amene akutayika, fungoli ndi la imfa, ndipo limaŵapha. Koma kwa amene akupulumuka, fungoli ndi la moyo, ndipo limaŵapatsa moyo. Nanga ndani angaithe ntchito yotere?

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Kwa amene akuwonongeka ndife fungo la imfa, limawapha. Ndipo kwa amene akupulumuka ndife fungo lamoyo, limawapatsa moyo. Ndani angayithe ntchito yotereyi?

Onani mutuwo



2 Akorinto 2:16
9 Mawu Ofanana  

ndipo mukakonzera Yehova nsembe yamoto, nsembe yopsereza, kapena yophera, pochita chowinda cha padera, kapena nsembe yaufulu, kapena nsembe ya pa nyengo zanu zoikika, kumchitira Yehova fungo lokoma, la ng'ombe kapena nkhosa;


Ndipo Simeoni anawadalitsa, nati kwa Maria amake, Taona, Uyu waikidwa akhale kugwa ndi kunyamuka kwa anthu ambiri mwa Israele; ndipo akhale chizindikiro chakutsutsana nacho;


Ndipo Yesu anati, Kudzaweruza ndadza Ine kudziko lino lapansi, kuti iwo osapenya apenye; ndi kuti iwo akupenya akhale osaona.


Koma ndi chisomo cha Mulungu ndili ine amene ndili; ndipo chisomo chake cha kwa ine sichinakhale chopanda pake, koma ndinagwirira ntchito yochuluka ya iwo onse; koma si ine, koma chisomo cha Mulungu chakukhala ndi ine.


Ndakhala wopanda nzeru, mwandichititsa kutero; pakuti inu munayenera kundivomereza; pakuti sindiperewere ndi atumwi oposatu m'kanthu konse, ndingakhale ndili chabe.