ndipo tigwiritsa ntchito, ndi kuchita ndi manja athu a ife tokha; polalatidwa tidalitsa; pozunzidwa, tipirira;
2 Akorinto 11:8 - Buku Lopatulika Ndinalanda za Mipingo ina, ndi kulandira kwa iwo kulipira kuti ndikatumikire inu; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndinalanda za Mipingo ina, ndi kulandira kwa iwo kulipira kuti ndikatumikire inu; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pakulandira zondithandiza kuchokera ku mipingo ina, ndidachita ngati kuŵalanda zao kuti ndikutumikireni inu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndinkalanda mipingo ina pomalandira thandizo kwa iwo kuti ndikutumikireni. |
ndipo tigwiritsa ntchito, ndi kuchita ndi manja athu a ife tokha; polalatidwa tidalitsa; pozunzidwa, tipirira;
ndipo pakukhala nanu, ndi kusowa, sindinasaukitse munthu aliyense; pakuti abale akuchokera ku Masedoniya, anakwaniritsa kusowa kwanga; ndipo m'zonse ndinachenjera ndekha, ndisalemetse inu, ndipo ndidzachenjerapo.
Koma ndili nazo zonse, ndipo ndisefukira; ndadzazidwa, popeza ndalandira kwa Epafrodito zija zidachokera kwanu, mnunkho wa fungo labwino, nsembe yolandirika, yokondweretsa Mulungu.