Ndipo Abrahamu anabwera kwa anyamata ake, ndipo anauka nayenda pamodzi kumuka ku Beereseba; ndipo anakhala Abrahamu pa Beereseba.
1 Samueli 8:2 - Buku Lopatulika Dzina la mwana wake woyamba ndiye Yowele, ndi dzina la wachiwiri ndiye Abiya; ndiwo oweruza a ku Beereseba. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Dzina la mwana wake woyamba ndiye Yowele, ndi dzina la wachiwiri ndiye Abiya; ndiwo oweruza a ku Beereseba. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mwana wake wachisamba anali Yowele, wachiŵiri anali Abiya. Iwoŵa ankaweruza ku Beereseba. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwana wake woyamba anali Yoweli, wachiwiri anali Abiya, ndipo ankaweruza ku Beeriseba. |
Ndipo Abrahamu anabwera kwa anyamata ake, ndipo anauka nayenda pamodzi kumuka ku Beereseba; ndipo anakhala Abrahamu pa Beereseba.
Ndipo Israele anamuka ulendo wake ndi zonse anali nazo, nafika ku Beereseba, napereka nsembe kwa Mulungu wa Isaki atate wake.
Ndipo iye ataona chimenechi, ananyamuka, nathawa kupulumutsa moyo, nafika ku Beereseba wa ku Yuda, nasiya mnyamata wake pamenepo.
koma musamafuna Betele, kapena kumalowa mu Giligala; musamapita ku Beereseba; pakuti Giligala adzalowadi m'ndende, ndi Betele adzasanduka chabe.