Amidiyani ndipo anamgulitsa iye anke ku Ejipito kwa Potifara, nduna ya Farao, kazembe wa alonda.
1 Samueli 8:15 - Buku Lopatulika Ndipo idzatenga limodzi la magawo khumi la mbeu zanu, ndi la minda yanu yampesa, nidzalipatsa akapitao ake, ndi anyamata ake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo idzatenga limodzi la magawo khumi la mbeu zanu, ndi la minda yanu yamphesa, nidzalipatsa akapitao ake, ndi anyamata ake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Idzalanda gawo lachikhumi la tirigu wanu ndi la mphesa zanu, nidzapatsa kwa akapitao ake ndi nduna zake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Idzatenga gawo lakhumi la tirigu wanu ndi mphesa zanu ndi kupereka kwa nduna zake ndi akapitawo ake. |
Amidiyani ndipo anamgulitsa iye anke ku Ejipito kwa Potifara, nduna ya Farao, kazembe wa alonda.
Ndipo ana ako amene adzabadwa ndi iwe, amene udzabala, iwo adzawatenga, ndipo adzakhala adindo m'chinyumba chake cha mfumu ya ku Babiloni.
Atatha masiku inanenawo mfumu kuti alowe nao, mkulu wa adindo analowa nao pamaso pa Nebukadinezara.
Ndipo mfumu inauza Asipenazi mkulu wa adindo kuti abwere nao ena a ana a Israele, a mbeu ya mafumu, ndi ya akalonga;
Ndipo idzalanda minda yanu, ndi minda ya mpesa yanu, ndi minda ya azitona, inde minda yoposayo, nidzaipatsa anyamata ake.
Ndipo idzatenga akapolo anu, ndi adzakazi anu, ndi anyamata anu okongola koposa, ndi abulu anu, nidzawagwiritsa ntchito yake.