Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 8:14 - Buku Lopatulika

14 Ndipo idzalanda minda yanu, ndi minda ya mpesa yanu, ndi minda ya azitona, inde minda yoposayo, nidzaipatsa anyamata ake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Ndipo idzalanda minda yanu, ndi minda ya mphesa yanu, ndi minda ya azitona, inde minda yoposayo, nidzaipatsa anyamata ake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Idzakulandani minda yanu yabwino kwambiri, minda yanu yamphesa ndi yaolivi, kudzanso minda yanu yazipatso, ndi kuipatsa nduna zake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Idzatenga minda yanu yabwino ya mpesa ndi ya mitengo ya olivi ndipo adzayipereka kwa antchito ake.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 8:14
7 Mawu Ofanana  

Ndipo uzilankhula naye, ndi kuti, Atero Yehova, Kodi wapha, nulandanso? Nulankhulenso naye, kuti, Atero Yehova, Paja agalu ananyambita mwazi wa Naboti pompaja agalu adzanyambita mwazi wako, inde wako.


Ndipo Ahabu analankhula ndi Naboti, nati, Ndipatse munda wako wampesa ukhale munda wanga wa ndiwo, popeza uli pafupi ndi nyumba yanga; ndipo m'malo mwake ndidzakupatsa munda wampesa wokoma woposa uwu; kapena kukakukomera ndidzakupatsa ndalama za pa mtengo wake.


Ndipo Yezebele mkazi wake anati kwa iye, Kodi mulamulira Aisraele tsopano ndinu? Taukani, idyani mkate, ukondwere mtima wanu; munda wa Naboti wa ku Yezireele ndidzakupatsani ndine.


Ndipo kalonga asatengeko cholowa cha anthu kuwazunza, ndi kulanda dziko laolao; apatse ana ake cholowa kulemba dziko lakelake, kuti anthu anga asabalalike, yense kuchoka m'dziko lake.


Ndipo Saulo anati kwa anyamata ake akuima chomzinga, Imvani tsopano, inu a Benjamini; kodi mwana wa Yese adzakupatsani inu nonse minda, ndi minda yampesa, kodi adzakuikani mukhale atsogoleri a zikwi ndi a mazana;


Ndipo idzatenga ana anu aakazi apange zonunkhira, naphikire, naumbe mikate.


Ndipo idzatenga limodzi la magawo khumi la mbeu zanu, ndi la minda yanu yampesa, nidzalipatsa akapitao ake, ndi anyamata ake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa