Ulimbike mtima, ndipo tichite chamuna lero chifukwa cha anthu athu ndi mizinda ya Mulungu wathu; Yehova nachite chomkomera.
1 Samueli 4:9 - Buku Lopatulika Limbikani, ndipo muchite chamuna, Afilisti inu, kuti mungakhale akapolo a Ahebri, monga iwowa anali akapolo anu. Chitani chamuna nimuponyane nao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Limbikani, ndipo muchite chamuna, Afilisti inu, kuti mungakhale akapolo a Ahebri, monga iwowa anali akapolo anu. Chitani chamuna nimuponyane nao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Limbani mtima, chitani chamuna, inu Afilisti, kuwopa kuti mungakhale akapolo a Ahebri, monga momwe iwowo analiri akapolo anu. Chitani chamuna, menyani nkhondo.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Limbani mtima Afilisti! Chitani chamuna, kuti mungakhale akapolo a Ahebri monga iwowa alili akapolo anu. Chitani chamuna ndipo menyani nkhondo!’ ” |
Ulimbike mtima, ndipo tichite chamuna lero chifukwa cha anthu athu ndi mizinda ya Mulungu wathu; Yehova nachite chomkomera.
Ndipo mitundu ya anthu idzawatenga, ndi kuwafikitsa kumalo a kwao; ndipo a nyumba ya Israele adzakhala nao amitunduwo m'dziko la Yehova, ndi kuwayesa atumiki ndi adzakazi, ndipo amitunduwo adzatengedwa ndende, ndi amenewo anali ndende zao; ndipo Aisraele adzalamulira owavuta.
Tsoka kwa iwe amene usakaza, chinkana sunasakazidwe; nupangira chiwembu, chinkana sanakupangire iwe chiwembu! Utatha kusakaza, iwe udzasakazidwa; ndipo utatha kupangira chiwembu, iwo adzakupangira iwe chiwembu.
Pamenepo mkwiyo wa Yehova unayakira Israele, nawagulitsa m'dzanja la Afilisti, ndi m'dzanja la ana a Amoni.
Ndipo ana a Israele anaonjeza kuchita choipa pamaso pa Yehova; nawapereka Yehova m'dzanja la Afilisti zaka makumi anai.
Ndiponso Ahebri akukhala nao Afilisti kale, amene anatuluka m'dziko lozungulira kukalowa nao kuzithando; iwonso anatembenukira kuti akakhale ndi Aisraele amene anali ndi Saulo ndi Yonatani.
Tsoka kwa ife! Adzatilanditsa ndani m'manja a milungu yamphamvu imeneyi? Milungu ija inakantha Aejipito ndi masautso onse m'chipululu ndi yomweyi.