1 Samueli 4:9 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero9 Limbani mtima Afilisti! Chitani chamuna, kuti mungakhale akapolo a Ahebri monga iwowa alili akapolo anu. Chitani chamuna ndipo menyani nkhondo!’ ” Onani mutuwoBuku Lopatulika9 Limbikani, ndipo muchite chamuna, Afilisti inu, kuti mungakhale akapolo a Ahebri, monga iwowa anali akapolo anu. Chitani chamuna nimuponyane nao. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20149 Limbikani, ndipo muchite chamuna, Afilisti inu, kuti mungakhale akapolo a Ahebri, monga iwowa anali akapolo anu. Chitani chamuna nimuponyane nao. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa9 Limbani mtima, chitani chamuna, inu Afilisti, kuwopa kuti mungakhale akapolo a Ahebri, monga momwe iwowo analiri akapolo anu. Chitani chamuna, menyani nkhondo.” Onani mutuwo |
Anthu a mitundu ina adzaperekeza a Israeli ku dziko lawo. Tsono Aisraeli adzasandutsa anthu a mitundu ina aja kukhala antchito awo aamuna ndi aakazi mʼdziko la Yehova. Ndiye kuti Aisraeli adzasandutsa akapolo anthu amene kale anali ambuye awo. Iwo adzasandutsa akapolo anthu amene kale ankawalamulira ndi kuwazunza.