Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




1 Samueli 4:8 - Buku Lopatulika

Tsoka kwa ife! Adzatilanditsa ndani m'manja a milungu yamphamvu imeneyi? Milungu ija inakantha Aejipito ndi masautso onse m'chipululu ndi yomweyi.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Tsoka kwa ife! Adzatilanditsa ndani m'manja a milungu yamphamvu imeneyi? Milungu ija inakantha Aejipito ndi masautso onse m'chipululu ndi yomweyi.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Tili m'mavuto! Angathe ndani kutipulumutsa kwa milungu yamphamvuyi? Imeneyitu ndi milungu ija idapha Aejipito ndi miliri ya mtundu uliwonse m'chipululu muja.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Atsoka ife! Adzatipulumutsa ndani mʼmanja mwa milungu yamphamvuyi? Iyi ndi milungu imene inakantha Aigupto ndi miliri yosiyanasiyana mʼchipululu.

Onani mutuwo



1 Samueli 4:8
8 Mawu Ofanana  

Mitundu ya anthu idamva, inanthunthumira; kuda mtima kwagwira anthu okhala mu Filistiya.


Ndipo Aejipito adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pakutambasula Ine dzanja langa pa Aejipito, ndikutulutsa ana a Israele pakati pao.


Pakuti nthawi ino ndidzatuma miliri yanga yonse pamtima pako, ndi pa anyamata ako, ndi pa anthu ako; kuti udziwe kuti palibe wina wonga Ine padziko lonse lapansi.


Izo zili nao ulamuliro wakutseka m'mwamba, isagwe mvula masiku a chinenero chao; ndipo ulamuliro zili nao pamadzi kuwasandutsa mwazi, ndi kupanda dziko ndi mliri uliwonse nthawi iliyonse zikafuna.


Ndipo Afilisti anaopa, pakuti anati, Mulungu wafika kuzithando. Ndipo iwo anati, Tsoka kwa ife! Popeza nkale lonse panalibe chinthu chotere.


Limbikani, ndipo muchite chamuna, Afilisti inu, kuti mungakhale akapolo a Ahebri, monga iwowa anali akapolo anu. Chitani chamuna nimuponyane nao.


Ndipo pamene anthu a ku Asidodi anaona kuti nchomwecho, anati iwowa, Likasa la Mulungu wa Israele lisakhalitse ndi ife; popeza dzanja lake litiwawira ife, ndi Dagoni mulungu wathu.