Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 15:14 - Buku Lopatulika

14 Mitundu ya anthu idamva, inanthunthumira; kuda mtima kwagwira anthu okhala mu Filistiya.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Mitundu ya anthu idamva, inanthunthumira; kuda mtima kwagwira anthu okhala m'Filistiya.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Anthu a mitundu ina amva mbiriyi, ndipo anjenjemera ndi mantha. Mantha oopsa aŵagwira Afilisti.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Anthu amitundu ina anamva za mbiriyi ndipo ananjenjemera ndi mantha, mantha woopsa agwira anthu a dziko la Filisiti.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 15:14
20 Mawu Ofanana  

Ndipo mbiri ya Davide inabuka m'maiko onse, nafikitsira Yehova kuopsa kwake pa amitundu onse.


Pomwepo anagwidwa nako kunthunthumira; anamva chowawa, ngati wam'chikuta.


Muswa zombo za ku Tarisisi ndi mphepo ya kum'mawa.


Usakondwere, iwe Filistiya, wonsewe, pothyoka ndodo inakumenya; pakuti m'muzu wa njoka mudzatuluka mphiri, ndimo chipatso chake chidzakhala njoka yamoto youluka.


Lira, chipata iwe; fuula, mzinda iwe; wasungunuka, Filistiya wonsewe, pakuti utsi uchokera kumpoto, ndipo palibe wosokera m'mizere yake.


Pofika mbiriyo ku Ejipito, iwo adzamva kuwawa kwambiri pa mbiri ya Tiro.


Ndidzavutanso mitima ya mitundu yambiri ya anthu, pakufikitsa Ine chionongeko chako mwa amitundu, m'maiko amene sunawadziwe.


Anaimirira, nandengulitsa dziko lapansi; anapenya, nanjenjemeretsa amitundu; ndi mapiri achikhalire anamwazika, zitunda za kale lomwe zinawerama; mayendedwe ake ndiwo a kale lomwe.


Ndinaona mahema a Kusani ali mkusauka; nsalu zotchinga za dziko la Midiyani zinanjenjemera.


ndipo adzawauza okhala m'dziko muno; adamva kuti inu Yehova muli pakati pa anthu awa; pakuti muoneka mopenyana, Yehova ndi mtambo wanu umaima pamwamba pao, ndipo muwatsogolera, ndi mtambo njo msana, ndi moto njo usiku.


Ndipo anatuma amithenga kwa Balamu mwana wa Beori, ku Petori, wokhala kumtsinje, wa dziko la anthu a mtundu wake, kuti amuitane, ndi kuti, Taonani, anatuluka anthu m'dziko la Ejipito; taonani, aphimba nkhope ya dziko, nakhala popenyana ndi ine.


Tsiku lino ndiyamba kuopsetsa nawe ndi kuchititsa mantha nawe anthu a pansi pa thambo lonse, amene adzamva mbiri yako, nadzanjenjemera, nadzawawidwa chifukwa cha iwe.


anaopa kwambiri, popeza Gibiyoni ndi mzinda waukulu, monga wina wa mizinda yachifumu, popezanso unaposa Ai kukula kwake, ndi amuna ake onse ndiwo amphamvu.


Ndipo titamva ichi mitima yathu inasungunuka; analibenso mtima ndi mmodzi yense, chifukwa cha inu; pakuti Yehova Mulungu wanu, ndiye Mulungu wa m'mwamba umo, ndi padziko lapansi.


Ndipo anamyankha Yoswa nati, Popeza anatiuzitsa akapolo anu kuti Yehova Mulungu wanu analamulira mtumiki wake Mose kukupatsani dziko lonseli, ndi kupasula nzika zonse za m'dziko pamaso panu; potero tinaopera kwambiri moyo wathu pamaso panu, ndipo tinachita chinthuchi.


Ndipo anati kwa iye, Akapolo anu afumira dziko la kutalitali, chifukwa cha dzina la Yehova Mulungu wanu; pakuti tidamva mbiri yake, ndi zonse anachita mu Ejipito,


Ndipo Afilisti anaopa, pakuti anati, Mulungu wafika kuzithando. Ndipo iwo anati, Tsoka kwa ife! Popeza nkale lonse panalibe chinthu chotere.


Tsoka kwa ife! Adzatilanditsa ndani m'manja a milungu yamphamvu imeneyi? Milungu ija inakantha Aejipito ndi masautso onse m'chipululu ndi yomweyi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa