Ndipo anyamata ake onse anapita naye limodzi; ndi Akereti ndi Apeleti, ndi Agiti onse, anthu mazana asanu ndi limodzi omtsata kuchokera ku Gati, anapita pamaso pa mfumu.
1 Samueli 27:4 - Buku Lopatulika Ndipo anauza Saulo kuti Davide anathawira ku Gati; ndipo iye sanamfunenso. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anauza Saulo kuti Davide anathawira ku Gati; ndipo iye sanamfunenso. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Saulo atamva kuti Davide wathaŵira ku Gati, sadamfunefunenso. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Sauli anamva kuti Davide wathawira ku Gati, ndipo sanamufunefunenso. |
Ndipo anyamata ake onse anapita naye limodzi; ndi Akereti ndi Apeleti, ndi Agiti onse, anthu mazana asanu ndi limodzi omtsata kuchokera ku Gati, anapita pamaso pa mfumu.
Pamenepo Saulo anati, Ndinachimwa; bwera, mwana wanga Davide; pakuti sindidzakuchitiranso choipa, popeza moyo wanga unali wa mtengo wapatali pamaso pako lero; ona, ndinapusa ndi kulakwa kwakukulu.
Ndipo Davide anakhala ndi Akisi ku Gati, iye ndi anthu ake, munthu yense ndi a pabanja pake, inde Davide ndi akazi ake awiri, Ahinowamu wa ku Yezireele, ndi Abigaile wa ku Karimele, mkazi wa Nabala.
Ndipo Davide anati kwa Akisi, Ngati mwandikomera mtima, andipatse malo kumudzi kwina kuminda, kuti ndikakhale kumeneko; pakuti mnyamata wanu adzakhala bwanji mu mzinda wachifumu pamodzi ndi inu?