1 Samueli 27:5 - Buku Lopatulika5 Ndipo Davide anati kwa Akisi, Ngati mwandikomera mtima, andipatse malo kumudzi kwina kuminda, kuti ndikakhale kumeneko; pakuti mnyamata wanu adzakhala bwanji mu mzinda wachifumu pamodzi ndi inu? Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20145 Ndipo Davide anati kwa Akisi, Ngati mwandikomera mtima, andipatse malo kumudzi kwina kumilaga, kuti ndikakhale kumeneko; pakuti mnyamata wanu adzakhala bwanji m'mudzi wachifumu pamodzi ndi inu? Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa5 Pambuyo pake Davide adauza Akisi kuti, “Ngati ndapeza kuyanja pamaso panu, mundipatse malo pa mudzi wina m'dziko mwanu kuti ndizikhala kumeneko. Kodi ine mtumiki wanu ndizikhaliranji pamodzi ndi inu mu mzinda wanu waufumu?” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero5 Kenaka Davide anawuza Akisi kuti, “Ngati ndapeza kuyanja pamaso panu mundipatse malo dera limodzi la dziko lanu kuti ndizikhala kumeneko. Mtumiki wanu adzakhala mu mzinda waufumu chifukwa chiyani?” Onani mutuwo |