1 Samueli 24:3 - Buku Lopatulika Ndipo panjira anafika ku makola a nkhosa, kumene kunali phanga; ndipo Saulo analowa kuti akadzithandize. Ndipo Davide ndi anyamata ake analikukhala m'kati mwa phangamo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo panjira anafika ku makola a nkhosa, kumene kunali phanga; ndipo Saulo analowa kuti akadzithandize. Ndipo Davide ndi anyamata ake analikukhala m'kati mwa phangamo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adafika ku makola a nkhosa a pamphepete pa njira, pamene panali phanga. Saulo adaloŵa m'phangamo kuti akadzithandize. Pamenepo nkuti Davide ndi anthu ake akubisala m'kati mwenimweni mwa phangalo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anafika ku makola a nkhosa amene anali mʼmbali mwa njira. Kumeneko kunali phanga, ndipo Sauli analowa mʼphangamo kuti akadzithandize. Davide ndi anthu ake ankabisala mʼkati mwenimweni mwa phangalo. |
Ndipo atatuluka iye, anadza akapolo ake; napenya, ndipo taonani pamakomo pa chipinda chosanja mpofungulira; nati iwo, Angophimba mapazi m'chipinda chake chosanja chopitidwa mphepo.
Pamenepo Saulo anadzisankhira anthu zikwi zitatu a Israele; zikwi za iwowa zinali ndi Saulo ku Mikimasi, ndi kuphiri la ku Betele; ndi chikwi chimodzi anali ndi Yonatani ku Gibea wa ku Benjamini; ndipo anawauza anthu ena onse amuke ku mahema ao.
Ndipo Saulo ananyamuka, natsikira chipululu cha Zifi, ndi anthu zikwi zitatu a Israele osankhika, kukafuna Davide m'chipululu cha Zifi.
Saulo namanga zithando m'phiri la Hakila kupenya kuchipululu kunjira. Koma Davide anakhala kuchipululu, naona kuti Saulo alikumfuna kuchipululu komweko.