1 Samueli 24:1 - Buku Lopatulika Ndipo kunali, pakubwerera Saulo potsata Afilisti, anamuuza, kuti, Taonani, Davide ali ku chipululu cha Engedi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo kunali, pakubwerera Saulo potsata Afilisti, anamuuza, kuti, Taonani, Davide ali ku chipululu cha Engedi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Saulo atabwerako kumene ankamenyana ndi Afilisti kuja, adamva kuti Davide ali ku chipululu cha Engedi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Sauli atabwera kuchokera kumene amathamangitsa Afilisti anamva kuti, “Davide ali mʼchipululu cha Eni Gedi.” |
Anthu oneneza anali mwa iwe, kuti akhetse mwazi; ndipo anadya pamapiri mwa iwe, pakati pa iwe anachita zamanyazi.
Ndipo kudzachitika, kuti asodzi adzaima komweko; kuyambira pa Engedi kufikira ku Enegilaimu kudzakhala poyanikira makoka; nsomba zao zidzakhala za mitundumitundu, ngati nsomba za mu Nyanja Yaikulu, zambirimbiri.
ndi Nibisani, ndi Mzinda wa Mchere, ndi Engedi; mizinda isanu ndi umodzi pamodzi ndi midzi yao.
Ndipo a ku Zifi anakwera kwa Saulo ku Gibea, nati, Davide salikubisala kwathu kodi, m'ngaka za m'nkhalango ku Horesi, m'phiri la Hakila, limene lili kumwera kwa chipululu?