1 Samueli 20:34 - Buku Lopatulika Pamenepo Yonatani anauka pagome wolunda ndithu, osadya kanthu tsiku lachiwiri la mwezi, pakuti mtima wake unali ndi chisoni chifukwa cha Davide, popeza atate wake anamchititsa manyazi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo Yonatani anauka pagome wolunda ndithu, osadya kanthu tsiku lachiwiri la mwezi, pakuti mtima wake unali ndi chisoni chifukwa cha Davide, popeza atate wake anamchititsa manyazi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Yonatani adanyamuka pa tebulo atakwiya koopsa, ndipo pa tsiku lachiŵiri la phwandolo sadadye. Adaavutika kwambiri mumtima mwake, chifukwa choti bambo wake adaachita Davide chipongwe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yonatani anachoka pa tebulopo ali wopsa mtima kwambiri. Tsiku lachiwiri la chikondwererocho Yonatani sanadye chakudya. Iye anawawidwa mtima chifukwa abambo ake anatsimikiza zakupha Davide. |
Ndipo m'mene anawaunguza ndi mkwiyo, ndi kumva chisoni chifukwa cha kuuma kwa mitima yao, ananena kwa munthuyo, Tambasula dzanja lako. Ndipo analitambasula; ndipo linachira dzanja lake.
Ndipo Saulo anamponyera mkondo kuti amgwaze; momwemo Yonatani anazindikira kuti atate wake anatsimikiza mtima kupha Davide.
Ndipo m'mawa, Yonatani ananka kuthengoko pa nthawi imene anapangana ndi Davide, ali ndi kamnyamata.