1 Samueli 17:10 - Buku Lopatulika Nati Mfilistiyo, Ine ndinyoza makamu a nkhondo a Israele lero; mundipatse munthu, kuti tilimbane ife awiri. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Nati Mfilistiyo, Ine ndinyoza makamu a nkhondo a Israele lero; mundipatse munthu, kuti tilimbane ife awiri. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tiwonane lero lino basi! Patseni munthu kuti ndimenyane naye.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Mfilisitiyo anati, “Bwerani lero timenyane basi! Patseni munthu kuti ndimenyane naye.” |
Ndipo wotsatana naye Eleazara mwana wa Dodo mwana wa Mwahohi, mmodzi wa ngwazi zitatu zokhala ndi Davide pamene iwo anatonza Afilisti osonkhanidwa kunkhondo kumeneko, atachoka Aisraele;
Kapena Yehova Mulungu wanu adzamva mau onse a kazembeyo, amene anamtuma mfumu ya Asiriya mbuye wake, kuti atonze Mulungu wamoyo, nadzamlanga chifukwa cha mau adawamva Yehova Mulungu wanu; chifukwa chake uwakwezere otsalawo pemphero.
Koma Sanibalati Muhoroni, ndi Tobiya kapolo Mwamoniyo, ndi Gesemu Mwarabu, anamva natiseka pwepwete, natipeputsa, nati, Chiyani ichi muchichita? Mulikupandukira mfumu kodi?
Atero Yehova, wanzeru asadzitamandire m'nzeru zake, wamphamvu asadzitamandire m'mphamvu yake, wachuma asadzitamandire m'chuma chake;
Tsono ine Nebukadinezara ndiyamika, ndi kukuza, ndi kulemekeza Mfumu ya Kumwamba, pakuti ntchito zake zonse nzoona, ndi njira zake chiweruzo; ndi oyenda m'kudzikuza kwao, Iye akhoza kuwachepetsa.
Ndipo pamene Saulo ndi Aisraele onse anamva mau ao a Mfilistiyo, anadodoma, naopa kwambiri.
Ine kapolo wanu ndinapha mkango ndi chimbalangondo zonse ziwiri; ndipo Mfilisti uyu wosadulidwa adzakhala ngati mmodzi wa izo, popeza wanyoza makamu a Mulungu wamoyo.
Ndipo Davide anati kwa Mfilistiyo, Iwe ukudza kwa ine ndi lupanga, ndi mkondo, ndi nthungo; koma ine ndafika kwa iwe m'dzina la Yehova wa makamu, Mulungu wa ankhondo a Israele amene iwe unawanyoza.