1 Samueli 16:6 - Buku Lopatulika Ndipo kunali, pakufika iwo, iye anayang'ana pa Eliyabu, nati, Zoonadi, wodzozedwa wa Yehova ali pamaso pake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo kunali, pakufika iwo, iye anayang'ana pa Eliyabu, nati, Zoonadi, wodzozedwa wa Yehova ali pamaso pake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Onsewo atafika, Samuele adayang'ana Eliyabu namaganiza kuti, “Ndithudi amene Chauta adamsankha ndi uyu ali pamaso pakeyu.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamene anafika, Samueli anaona Eliabu ndipo anaganiza “Ndithu wodzozedwa wa Yehova uja ndi uyu wayima pamaso pakeyu.” |
ndi Yese anabala mwana wake wamwamuna woyamba Eliyabu, ndi Abinadabu wachiwiri, ndi Simea wachitatu,
Komatu Yehova Mulungu wa Israele anasankha ine m'nyumba yonse ya atate wanga, ndikhale mfumu ya Israele kosatha; pakuti anasankhiratu Yuda akhale mtsogoleri, ndi m'nyumba ya Yuda nyumba ya atate wanga, ndi mwa ana a atate wanga ndinamkomera ndine, andilonge ufumu wa Israele yense;
Ndipo Rehobowamu anadzitengera mkazi Mahalati, mwana wamkazi wa Yerimoti mwana wa Davide, ndi wa Abihaili mwana wamkazi wa Eliyabu mwana wa Yese;
Pamenepo anati kwa Zeba ndi Zalimuna, Amunawo munawapha ku Tabori anali otani? Iwo nayankha, Monga iwe momwemo iwowa; yense wakunga mwana wa mfumu.
Ndipo ana atatu aakulu a Yese anatsata Saulo kunkhondoko; ndi maina ao a ana ake atatuwo adapita ku nkhondowo ndiwo Eliyabu woyambayo, ndi mnzake womponda pamutu pake Abinadabu, ndi wachitatu Sama.
Ndipo Davide anasiya akatundu ake m'dzanja la wosungira akatundu, nathamangira ku khamulo, nadza nawalonjera abale ake.