1 Samueli 17:13 - Buku Lopatulika13 Ndipo ana atatu aakulu a Yese anatsata Saulo kunkhondoko; ndi maina ao a ana ake atatuwo adapita ku nkhondowo ndiwo Eliyabu woyambayo, ndi mnzake womponda pamutu pake Abinadabu, ndi wachitatu Sama. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201413 Ndipo ana atatu akulu a Yese anatsata Saulo kunkhondoko; ndi maina ao a ana ake atatuwo adapita ku nkhondowo ndiwo Eliyabu woyambayo, ndi mnzake womponda pamutu pake Abinadabu, ndi wachitatu Sama. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa13 Ana ake aamuna anali aŵa: Eliyabu mwana wake wachisamba, wachiŵiri Abinadabu, ndipo wachitatu anali Sama. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero13 Ana atatu oyamba kubadwa a Yese nʼkuti atapita nawo ku nkhondo pamodzi ndi Sauli. Woyamba dzina lake anali Eliabu, wachiwiri anali Abinadabu, ndipo wachitatu anali Sama. Onani mutuwo |