1 Samueli 15:6 - Buku Lopatulika Ndipo Saulo anauza Akeni kuti, Mukani, chokani mutsike kutuluka pakati pa Aamaleke, kuti ndingakuonongeni pamodzi ndi iwo; pakuti inu munachitira ana a Israele onse zabwino, pakufuma iwo ku Ejipito. Chomwecho Akeni anachoka pakati pa Aamaleke. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Saulo anauza Akeni kuti, Mukani, chokani mutsike kutuluka pakati pa Aamaleke, kuti ndingakuonongeni pamodzi ndi iwo; pakuti inu munachitira ana a Israele onse zabwino, pakufuma iwo ku Ejipito. Chomwecho Akeni anachoka pakati pa Aamaleke. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono adauza Akeni kuti, “Muchoke pakati pa Aamaleke, kuti ndingakuwonongereni kumodzi. Pakuti inu mudachitira chifundo Aisraele muja ankachokera ku Ejipitomu.” Motero Akeni adachoka pakati pa Aamaleke. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono Sauli anawuza Akeni kuti, “Samukani, muchoke pakati pa Aamaleki kuti ine ndisakuwonongeni pamodzi ndi iwo pakuti inu munaonetsa kukoma mtima kwa Aisraeli onse pamene ankatuluka mʼdziko la Igupto,” Choncho Akeni anachoka pakati pa Aamaleki. |
Musamatero ai, kupha olungama pamodzi ndi oipa, kuta olungama akhale monga oipa; musamatero ai; kodi sadzachita zoyenera woweruza wa dziko lonse lapansi?
Ndi mabanja a alembi okhala ku Yabezi: Atirati, Asimeati, Asukati. Iwo ndiwo Akeni ofuma ku Hamati, kholo la nyumba ya Rekabu.
Tamvera mau anga tsopano, ndikupangire nzeru, ndi Mulungu akhale nawe; ukhale m'malo mwa anthu kwa Mulungu, nupite nayo milandu kwa Mulungu;
Ndipo Aisraele onse akukhala pozinga pao anathawa pakumva kufuula kwao; pakuti anati, Lingatimeze dziko ifenso.
Ndipo ndi mau ena ambiri anachita umboni, nawadandaulira iwo, nanena, Mudzipulumutse kwa mbadwo uno wokhotakhota.
Chifukwa chake, Tulukani pakati pao, ndipo patukani, ati Ambuye, Ndipo musakhudza kanthu kosakonzeka; ndipo Ine ndidzalandira inu,
Ambuye achitire banja la Onesifore chifundo; pakuti anatsitsimutsa ine kawirikawiri, ndipo sanachite manyazi ndi unyolo wanga;
Ndipo zokhumbitsa moyo wako zidakuchokera; ndipo zonse zolongosoka, ndi zokometsetsa zakutayikira, ndipo izi sudzazipezanso konse.
Ndipo ana a Mkeni mlamu wake wa Mose, anakwera kutuluka m'mzinda wa m'migwalangwa pamodzi ndi ana a Yuda, nalowa m'chipululu cha Yuda chokhala kumwera kwa Aradi; namuka iwo nakhala ndi anthuwo.
Ndipo Hebere Mkeni anadzisiyanitsa ndi Akeni, ndi ana a Hobabu mlamu wake wa Mose, namanga mahema ake mpaka thundu wa mu Zaananimu, ndiwo wa ku Kedesi.
Wodalitsika, woposa akazi, akhale Yaele mkazi wa Hebere Mkeni. Akhale wodalitsika woposa akazi a m'hema.
Ndipo Akisi anati, Waponyana nkhondo ndi yani lero? Nati Davide, Ndi a kumwera kwa Ayuda, ndi a kumwera kwa Ayerameele, ndi a kumwera kwa Akeni.
ndi kwa iwo a ku Rakala, ndi kwa iwo a ku m'mizinda ya Ayerameele, ndi kwa iwo a m'mizinda ya Akeni;