Ndipo anatenga amuna ngati zikwi zisanu, nawaika m'molalira pakati pa Betele ndi Ai, kumadzulo kwa mzinda.
1 Samueli 15:5 - Buku Lopatulika Ndipo Saulo anafika kumzinda wa Amaleke, nalalira kuchigwa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Saulo anafika kumudzi wa Amaleke, nalalira kuchigwa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo Saulo adafika ku mzinda wa Aamaleke, naubisalira m'khwaŵa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Sauli anapita ku mzinda wa Aamaleki nawubisalira mʼkhwawa. |
Ndipo anatenga amuna ngati zikwi zisanu, nawaika m'molalira pakati pa Betele ndi Ai, kumadzulo kwa mzinda.
nawalamulira ndi kuti, Taonani, muzikhala olalira kukhonde kwa mzinda; musakhalira kutali ndi mzinda, koma mukhale okonzekeratu nonse;
Ndipo Saulo anamemeza anthu, nawawerenga ku Telaimu, akuyenda pansi zikwi mazana awiri, ndi a kwa Yuda anthu zikwi khumi.
Ndipo Saulo anauza Akeni kuti, Mukani, chokani mutsike kutuluka pakati pa Aamaleke, kuti ndingakuonongeni pamodzi ndi iwo; pakuti inu munachitira ana a Israele onse zabwino, pakufuma iwo ku Ejipito. Chomwecho Akeni anachoka pakati pa Aamaleke.