Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yoswa 8:12 - Buku Lopatulika

12 Ndipo anatenga amuna ngati zikwi zisanu, nawaika m'molalira pakati pa Betele ndi Ai, kumadzulo kwa mzinda.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ndipo anatenga amuna ngati zikwi zisanu, nawaika m'molalira pakati pa Betele ndi Ai, kumadzulo kwa mudzi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Yoswa adapatula anthu zikwi zisanu, naŵabisa cha kuzambwe kwa mzindawo, pakati pa Ai ndi Betele.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Yoswa anali atatenga asilikali 5,000 ndi kuwabisa pakati pa Ai ndi Beteli, kumadzulo kwa mzindawo.

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 8:12
7 Mawu Ofanana  

Ndipo iye anachoka kumeneko kunka kuphiri la kum'mawa kwa Betele, namanga hema wake; Betele anali kumadzulo, ndi Ai anali kum'mawa: kumeneko ndipo anammangira Yehova guwa la nsembe, naitanira dzina la Yehova.


Ndipo anatcha dzina la pamenepo Betele; pakuyamba dzina lake la mzindawo ndi Luzi.


Ndi anthu onse a nkhondo okhala naye anakwera, nayandikira nafika pamaso pa mzinda, namanga misasa kumpoto kwa Ai; koma pakati pa iye ndi Ai panali chigwa.


Momwemo anaika anthu, khamu lonse lokhala kumpoto kwa mzinda, ndi olalira ao kumadzulo kwa mzinda, ndipo usiku uja Yoswa analowa pakati pa chigwa.


Ndipo anakwera iwo a m'nyumba ya Yosefe, naonso kunka ku Betele; ndipo Yehova anakhala nao.


Ndipo Saulo anafika kumzinda wa Amaleke, nalalira kuchigwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa