Ndipo Mose ananena ndi anthu, Musaope, chilimikani, ndipo penyani chipulumutso cha Yehova, chimene adzakuchitirani lero; pakuti Aejipito mwawaona lerowa, simudzawaonanso konse.
1 Samueli 12:16 - Buku Lopatulika Chifukwa chake tsono, imani pano, muone chinthu ichi chachikulu Yehova adzachichita pamaso panu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chifukwa chake tsono, imani pano, muone chinthu ichi chachikulu Yehova adzachichita pamaso panu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nchifukwa chake tsono imani pomwepa, muwone chinthu chachikulu chimene Chauta akuchitireni mukupenya. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Tsono imani pomwepa kuti muone chinthu chachikulu chimene Yehova ali pafupi kuchita pamaso panu! |
Ndipo Mose ananena ndi anthu, Musaope, chilimikani, ndipo penyani chipulumutso cha Yehova, chimene adzakuchitirani lero; pakuti Aejipito mwawaona lerowa, simudzawaonanso konse.
Ndipo Israele anaiona ntchito yaikulu imene Yehova anachitira Aejipito, ndipo anthuwo anaopa Yehova; nakhulupirira Yehova ndi mtumiki wake Mose.
Chifukwa chake tsono, imani pano, kuti ndiweruzane nanu pamaso pa Yehova, za ntchito zonse zolungama za Yehova anakuchitirani inu ndi makolo anu.
Pomwepo Samuele ananena ndi Saulo, Imani, ndidzakudziwitsani chimene Yehova wanena ndi ine usiku walero. Ndipo iyeyo anati kwa iye, Nenani.