Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 12:17 - Buku Lopatulika

17 Si nyengo yakumweta tirigu lero kodi? Ndidzaitana kwa Yehova, kuti atumize bingu ndi mvula; ndipo mudzazindikira ndi kuona kuti choipa chanu munachichita pamaso pa Yehova ndi kudzipemphera mfumu, nchachikulu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Si nyengo yakumweta tirigu lero kodi? Ndidzaitana kwa Yehova, kuti atumize bingu ndi mvula; ndipo mudzazindikira ndi kuona kuti choipa chanu munachichita pamaso pa Yehova ndi kudzipemphera mfumu, nchachikulu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Kodi ino si nthaŵi yachilimwe yodula tirigu? Komabe nditama Chauta mopemba kuti agwetse mvula yamabingu. Apo mudziŵa ndi kuwona kuti tchimo lanu limene mwachita popempha mfumu kwa Chauta nlalikulu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Kodi ino si nthawi yokolola tirigu? Komabe ndipemphera kwa Yehova kuti agwetse mvula ya mabingu. Zikatero mudzadziwa kuti tchimo lanu limene mwachita popempha mfumu kwa Yehova ndi lalikulu.”

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 12:17
13 Mawu Ofanana  

Mwa ansembe ake muli Mose ndi Aroni, ndi Samuele mwa iwo akuitanira dzina lake; anaitana kwa Yehova, ndipo Iye anawayankha.


Ndipo kunali m'mawa mwake, kuti Mose anati kwa anthu, Mwachimwa kuchimwa kwakukulu; koma ndikwera kwa Yehova tsopano, kapena ndidzachita chotetezera uchimo wanu.


Monga chipale chofewa m'malimwe, ndi mvula m'masika, momwemo ulemu suyenera chitsiru.


Ndipo Yehova anati kwa ine, Ngakhale Mose ndi Samuele akadaima pamaso panga, koma mtima wanga sukadasamalira anthu awa; muwachotse iwo pamaso panga, atuluke.


Pomwepo Yoswa ananena kwa Yehova tsiku limene Yehova anapereka Aamori pamaso pa ana a Israele; ndipo anati pamaso pa Israele, Dzuwa iwe, linda, pa Gibiyoni, ndi Mwezi iwe, m'chigwa cha Ayaloni.


Chifukwa chake siyi mfumu imene munaisankha, imene munandipempha; ndipo taonani, Yehova anakuikirani mfumu.


Ndipo anthu onse ananena ndi Samuele, Mupempherere akapolo anu kwa Yehova Mulungu wanu, kuti tingafe; popeza pamwamba pa zoipa zathu zonse tinaonjeza choipa ichi, chakuti tinadzipemphera mfumu.


Otsutsana ndi Yehova adzaphwanyika; kumwamba Iye adzagunda pa iwo; Yehova adzaweruza malekezero a dziko. Ndipo adzapatsa mphamvu mfumu yake, nadzakweza nyanga ya wodzozedwa wake.


Ndipo Samuele anati, Musonkhanitse Aisraele onse ku Mizipa, ndipo ine ndidzakupemphererani kwa Yehova.


Koma chimenechi sichinakondweretse Samuele, pamene iwo anati, Tipatseni mfumu kuti itiweruze. Ndipo Samuele anapemphera kwa Yehova.


Ndipo Yehova ananena ndi Samuele, Umvere mau onse anthuwo alikulankhula nawe; popeza sindiwe anakukana, koma ndine anandikana, kuti ndisakhale mfumu yao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa