Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 15:16 - Buku Lopatulika

16 Pomwepo Samuele ananena ndi Saulo, Imani, ndidzakudziwitsani chimene Yehova wanena ndi ine usiku walero. Ndipo iyeyo anati kwa iye, Nenani.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Pomwepo Samuele ananena ndi Saulo, Imani, ndidzakudziwitsani chimene Yehova wanena ndi ine usiku walero. Ndipo iyeyo anati kwa iye, Nenani.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Apo Samuele adamuuza kuti, “Basi, musapitirize! Imani ndikukambireni zimene Chauta wandiwuza usiku.” Tsono Saulo adati, “Nenani.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Koma Samueli anati kwa Sauli, “Khala chete! Ima ndikuwuze zimene Yehova wandiwuza usiku wathawu.” Sauli anayankha kuti, “Ndiwuzeni.”

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 15:16
8 Mawu Ofanana  

Ndipo kunachitika, pamene Ahiya anamva mgugu wa mapazi ake alinkulowa pakhomo, anati, Lowa mkazi iwe wa Yerobowamu, wadzizimbaitsiranji? Pakuti ine ndatumidwa kwa iwe ndi mau olasa.


Ndipo mfumu inati, Ndikulumbiritse kangati kuti undiuze zoona zokhazokha m'dzina la Yehova?


Ndipo Yesaya anati kwa Hezekiya, Imvani mau a Yehova wa makamu.


Ndipo Yeremiya mneneri ananena mau onsewa kwa Zedekiya mfumu ya Yuda mu Yerusalemu,


Chifukwa chake tsono, imani pano, kuti ndiweruzane nanu pamaso pa Yehova, za ntchito zonse zolungama za Yehova anakuchitirani inu ndi makolo anu.


Ndipo Saulo anati, Anazitenga kwa Aamaleke; pakuti anthu anasunga nkhosa zokometsetsa ndi ng'ombe, kuzipereka nsembe kwa Yehova Mulungu wanu; koma zina tinaziononga konsekonse.


Nati Samuele, M'mene munali wamng'ono m'maso a inu nokha, kodi simunaikidwe mutu wa mafuko a Israele? Ndipo Yehova anakudzozani mfumu ya Israele.


Ndipo pamene analikutsika polekeza mzinda, Samuele ananena ndi Saulo, Uzani mnyamatayo abatsogola; napita iyeyo. Koma inu muime pano, kuti ndikumvetseni mau a Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa