Ndipo Yowabu anapereka kwa mfumu kuchuluka kwa anthu adawawerenga; ndipo mu Israele munali anthu zikwi mazana asanu ndi atatu, ngwazi zosolola lupanga; ndi anthu a Yuda ndiwo zikwi mazana asanu.
1 Samueli 11:8 - Buku Lopatulika Ndipo anawawerenga ku Bezeki; ndipo ana a Israele anali zikwi mazana atatu, ndi anthu a Yuda ndiwo zikwi makumi atatu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anawawerenga ku Bezeki; ndipo ana a Israele anali zikwi mazana atatu, ndi anthu a Yuda ndiwo zikwi makumi atatu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Saulo adaŵasonkhanitsa ku Bezeki, naŵaŵerenga. Aisraele analipo 300,000, Ayuda analipo 30,000. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamenepo Sauli anawasonkhanitsa ku Bezeki nawawerenga, ndipo Aisraeli analipo 300,000, Ayuda analipo 30,000. |
Ndipo Yowabu anapereka kwa mfumu kuchuluka kwa anthu adawawerenga; ndipo mu Israele munali anthu zikwi mazana asanu ndi atatu, ngwazi zosolola lupanga; ndi anthu a Yuda ndiwo zikwi mazana asanu.
Ndipo akulu a anthu onse a mafuko onse a Israele anadziimika mu msonkhano wa anthu a Mulungu, anthu oyenda pansi zikwi mazana anai akusolola lupanga.
Ndipo anati kwa mithenga inadzayi, Muzitero kwa anthu a ku Yabesi-Giliyadi, Mawa litatentha dzuwa, mudzaona chipulumutso. Ndipo mithenga inadza niuza a ku Yabesi; nakondwera iwowa.
Ndipo Samuele anauka nachoka ku Giligala kunka ku Gibea wa ku Benjamini. Ndipo Saulo anawerenga anthu amene anali naye, monga mazana asanu ndi limodzi.
Ndipo Saulo anamemeza anthu, nawawerenga ku Telaimu, akuyenda pansi zikwi mazana awiri, ndi a kwa Yuda anthu zikwi khumi.