Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Mafumu 3:6 - Buku Lopatulika

6 Ndipo mfumu Yehoramu anatuluka mu Samariya nthawi yomweyo, namemeza Aisraele onse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ndipo mfumu Yehoramu anatuluka m'Samariya nthawi yomweyo, namemeza Aisraele onse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Motero mwamsangamsanga mfumu Yoramu adatuluka kuchoka ku Samariya, nasonkhanitsa gulu lonse la ankhondo la Aisraele.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Choncho nthawi imeneyi mfumu Yoramu inatuluka mu Samariya ndi kukasonkhanitsa Aisraeli onse.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 3:6
6 Mawu Ofanana  

Ndipo Aisraele anamemezananso, anali naye kamba, nakakomana nao; ndipo Aisraele anamanga misasa yao pandunji pao, ngati timagulu tiwiri ta anaambuzi; koma Aaramu anadzaza dziko.


Koma kunachitika, atafa Ahabu mfumu ya Mowabu anapandukana ndi mfumu ya Israele.


Nakatumiza mau kwa Yehosafati mfumu ya Yuda, ndi kuti, Mfumu ya Mowabu wapandukana ndi ine; kodi udzamuka nane kukathira nkhondo pa Mowabu? Nati, Ndidzakwera: ine ndikhala ngati iwe, anthu anga ngati anthu ako, akavalo anga ngati akavalo ako.


Ndipo anawawerenga ku Bezeki; ndipo ana a Israele anali zikwi mazana atatu, ndi anthu a Yuda ndiwo zikwi makumi atatu.


Ndipo Saulo anamemeza anthu, nawawerenga ku Telaimu, akuyenda pansi zikwi mazana awiri, ndi a kwa Yuda anthu zikwi khumi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa