2 Mafumu 3:7 - Buku Lopatulika7 Nakatumiza mau kwa Yehosafati mfumu ya Yuda, ndi kuti, Mfumu ya Mowabu wapandukana ndi ine; kodi udzamuka nane kukathira nkhondo pa Mowabu? Nati, Ndidzakwera: ine ndikhala ngati iwe, anthu anga ngati anthu ako, akavalo anga ngati akavalo ako. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20147 Nakatumiza mau kwa Yehosafati mfumu ya Yuda, ndi kuti, Mfumu ya Mowabu wapandukana ndi ine; kodi udzamuka nane kukathira nkhondo pa Mowabu? Nati, Ndidzakwera: ine ndikhala ngati iwe, anthu anga ngati anthu ako, akavalo anga ngati akavalo ako. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa7 Kenaka Yoramuyo adatumiza mau kwa Yehosafati, mfumu ya ku Yuda, kuti, “Mfumu ya Amowabu yandigalukira ine. Kodi sungapite nane kunkhondo, kuti tikamenyane ndi Amowabu?” Tsono Yehosafatiyo adayankha kuti, “Ndidzapita. Ine ndi iwe ndife amodzi, anthu anga ndi ako omwe, akavalo anga ndi akonso.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero7 Yoramu anatumizanso uthenga uwu kwa Yehosafati mfumu ya ku Yuda: “Mfumu ya ku Mowabu yandiwukira. Kodi ungapite nane kukamenyana ndi Mowabu?” Iye anayankha kuti, “Ine ndidzapita nawe. Iwe ndi ine ndife anthu amodzi, anthu anga ali ngati anthu ako, akavalo anga ali ngati akavalo ako.” Onani mutuwo |