Ndipo Mulungu anamva mau a mnyamatayo, ndi mthenga wa Mulungu anamuitana Hagara, ndi mau odzera kumwamba, nati kwa iye, Watani Hagara? Usaope; chifukwa Mulungu anamva mau a mnyamata kumene ali.
1 Samueli 11:5 - Buku Lopatulika Ndipo, onani, Saulo anachokera kumunda alikutsata ng'ombe; nati Saulo, Choliritsa anthu misozi nchiyani? Ndipo anamuuza mau a anthu a ku Yabesi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo, onani, Saulo anachokera kumunda alikutsata ng'ombe; nati Saulo, Choliritsa anthu misozi nchiyani? Ndipo anamuuza mau a anthu a ku Yabesi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nthaŵi imeneyo nkuti Saulo akuchokera ku munda, akuyenda pambuyo pa ng'ombe zantchito. Tsono adafunsa kuti, “Chaŵavuta anthu nchiyani kuti azilira?” Pamenepo adamuuza nkhani ya anthu a ku Yabesi ija. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pa nthawiyo nʼkuti Sauli akubwera kuchokera ku munda, ali pambuyo pa ngʼombe zake za ntchito ndipo anafunsa. “Nʼchiyani chawavuta anthuwa kuti azilira motere?” Ndipo anamufotokozera zomwe anthu a mu mzinda wa Yabesi ananena. |
Ndipo Mulungu anamva mau a mnyamatayo, ndi mthenga wa Mulungu anamuitana Hagara, ndi mau odzera kumwamba, nati kwa iye, Watani Hagara? Usaope; chifukwa Mulungu anamva mau a mnyamata kumene ali.
Tsono anachokako, napeza Elisa mwana wa Safati alikukoketsa chikhasu ng'ombe ziwiriziwiri magoli khumi ndi awiri, iye yekha anakhala pa goli lakhumi ndi chiwiri; ndipo Eliya ananka kunali iyeyo, naponya chofunda chake pa iye.
Anamtenga kuja anatsata zoyamwitsa, awete Yakobo, anthu ake, ndi Israele, cholowa chake.
Ndipo anafuula kwa ana a Dani. Nacheuka iwo nati kwa Mika, Chakusowa chiyani, kuti wamemeza anthu ako?
Ndipo panali munthu Mbenjamini, dzina lake ndiye Kisi, mwana wa Abiyele, mwana wa Zerori, mwana wa Bekorati, mwana wa Afiya, mwana wa Mbenjamini, ndiye ngwazi.