Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 78:71 - Buku Lopatulika

71 Anamtenga kuja anatsata zoyamwitsa, awete Yakobo, anthu ake, ndi Israele, cholowa chake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

71 Anamtenga kuja anatsata zoyamwitsa, awete Yakobo, anthu ake, ndi Israele, cholandira chake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

71 Adamtenga kumene ankaŵeta nkhosa zimene zinali ndi ana, kuti adzakhale mbusa wa Yakobe, fuko lake, wa Israele, choloŵa chake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

71 kuchokera koyangʼanira nkhosa anamubweretsa kuti akhale mʼbusa wa anthu ake, Yakobo, wa Israeli cholowa chake.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 78:71
19 Mawu Ofanana  

Ndipo anati kwa iye, Mbuyanga adziwa kuti ana ali anthete, ndipo nkhosa ndi zoweta ndili nazo zilinkuyamwitsa: ndipo akathamangitsa tsiku limodzi zoweta zonse zidzafa.


Ine ndine wa awo amene ali amtendere ndi okhulupirika mu Israele; inu mulikufuna kuononga mzinda ndi mai wa mu Israele; mudzamezeranji cholowa cha Yehova?


Ndipo Davide analankhula ndi Yehova pamene anaona mthenga wakudwalitsa anthu, nati, Onani ndachimwa ine, ndinachita mwamphulupulu; koma nkhosa izi zinachitanji? Dzanja lanu likhale pa ine ndi pa nyumba ya atate wanga.


Masiku anapitawo, pamene Saulo anali mfumu yathu, inu ndinu amene munatsogolera Aisraele kutuluka nao ndi kubwera nao; ndipo Yehova ananena nanu, Uzidyetsa anthu anga Israele, ndi kukhala mtsogoleri wa Israele.


Chifukwa chake tsono udzatero kwa mtumiki wanga Davide, Atero Yehova wa makamu, Ndinakuchotsa kubusako kumene unalikutsata nkhosa kuti udzakhale mfumu ya anthu anga, ndiwo Israele.


Ngakhale kale lomwe, pokhala mfumu Sauloyo, wotuluka ndi kulowa nao Aisraele ndinu; ndipo Yehova Mulungu wanu anati kwa inu, Uzidyetsa anthu anga Aisraele, nukhale mtsogoleri wa anthu anga Israele.


Pulumutsani anthu anu, ndi kudalitsa cholowa chanu; muwawetenso, ndi kuwanyamula nthawi zonse.


Iye adzadyetsa zoweta zake ngati mbusa, nadzasonkhanitsa anaankhosa m'manja mwake, nadzawatengera pa chifuwa chake, ndipo adzatsogolera bwinobwino zimene ziyamwitsa.


Ndipo iwe Betelehemu, dziko la Yudeya, sukhala konse wamng'onong'ono mwa akulu a Yudeya. Pakuti Wotsogolera adzachokera mwa iwe, amene adzaweta anthu anga Aisraele.


Wetani gulu la Mulungu lili mwa inu, ndi kuliyang'anira, osati mokakamiza, koma mwaufulu, kwa Mulungu; osatsata phindu lonyansa, koma mwachangu;


Pamenepo Samuele anatenga nsupa ya mafuta, nawatsanulira pamutu pake, nampsompsona iye, nati, Sanakudzozeni ndi Yehova kodi, Mukhale mfumu ya pa cholowa chake?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa